Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




2 Mbiri 3:11 - Buku Lopatulika

11 Ndi mapiko a akerubi m'litali mwake ndimo mikono makumi awiri; phiko la kerubi mmodzi mikono isanu, lojima khoma la nyumba; ndi phiko linzake mikono isanu, lokhudzana nalo phiko la kerubi wina.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

11 Ndi mapiko a akerubi m'litali mwake ndimo mikono makumi awiri; phiko la kerubi mmodzi mikono isanu, lojima khoma la nyumba; ndi phiko linzake mikono isanu, lokhudzana nalo phiko la kerubi wina.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

11 Mapiko a akerubiwo akaŵatambasula, pamodzi ankakwanira mamita asanu ndi anai. Phiko limodzi la kerubi mmodzi, la mamita aŵiri nkanthu, linkakhudza ku khoma la nyumba. Phiko lake lina, nalonso la mamita aŵiri nkanthu, linkakhudzana ndi phiko la kerubi mnzake.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

11 Kutalika kwa mapiko onse a Akerubi kunali mamita asanu ndi anayi. Phiko la Kerubi woyamba linali loposerapo mamita awiri ndipo limakhudza khoma la Nyumba ya Mulungu, pamene phiko linalo, lotalikanso koposerapo mamita awiri, limakhudza phiko la Kerubi winayo.

Onani mutuwo Koperani




2 Mbiri 3:11
4 Mawu Ofanana  

Ndipo anaika akerubiwo m'chipinda cha m'katimo, ndi mapiko a akerubiwo anatambasuka kotero kuti phiko lake la kerubi mmodzi linajima ku khoma limodzi, ndipo phiko la kerubi wina linajima khoma lina, ndi mapiko ao anagundana pakati pa nyumba.


Ndipo m'malo opatulika kwambiri anapanga akerubi awiri, anachita osema, nawakuta ndi golide.


Ndi phiko la kerubi wina mikono isanu lojima khoma la nyumba, ndi phiko linzake mikono isanu lolumikizana ndi phiko la kerubi wina.


Mapiko ao analumikizana; sizinatembenuke poyenda; chilichonse chinayenda ndi kulunjika kutsogoloko.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa