2 Mbiri 27:5 - Buku Lopatulika5 Anayambananso ndi mfumu ya ana a Amoni, namgonjetsa. Ndi ana a Amoni anamninkha chaka chomwechi matalente a siliva zana limodzi, ndi miyeso ya tirigu zikwi khumi, ndi ya barele zikwi khumi. Ana a Amoni anabwera nazo zomwezo kwa iye chaka chachiwiri ndi chachitatu chomwe. Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 20145 Anayambananso ndi mfumu ya ana a Amoni, namgonjetsa. Ndi ana a Amoni anamninkha chaka chomwechi matalente a siliva zana limodzi, ndi miyeso ya tirigu zikwi khumi, ndi ya barele zikwi khumi. Ana a Amoni anabwera nazo zomwezo kwa iye chaka chachiwiri ndi chachitatu chomwe. Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa5 Adamenyana nkhondo ndi mfumu ya Aamoni, ndipo adaŵagonjetsa Aamoniwo. Nchifukwa chake, chaka choyamba Aamoni aja adapereka makilogramu 3,400 a siliva, matani 1,000 a tirigu, ndiponso matani 1,000 a barele. Aamoni ankalipira kwa Yotamuyo zinthu zonga zomwezo pa chaka chachiŵiri ndi chachitatu. Onani mutuwoMawu a Mulungu mu Chichewa Chalero5 Yotamu anachita nkhondo ndi mfumu ya Aamoni ndipo anawagonjetsa. Chaka chimenecho Aamoni anapereka makilogalamu 3,400, matani 1,000 a tirigu ndiponso matani 1,000 a barele. Aamoni anabweretsa zinthu zomwezi chaka chachiwiri ndi chachitatu. Onani mutuwo |