Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




2 Mbiri 27:1 - Buku Lopatulika

1 Yotamu anali wa zaka makumi awiri, mphambu zisanu polowa ufumu wake, nakhala mfumu mu Yerusalemu zaka khumi ndi zisanu ndi chimodzi; ndi dzina la make ndiye Yerusa mwana wa Zadoki.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

1 Yotamu anali wa zaka makumi awiri, mphambu zisanu polowa ufumu wake, nakhala mfumu m'Yerusalemu zaka khumi ndi zisanu ndi chimodzi; ndi dzina la make ndiye Yerusa mwana wa Zadoki.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

1 Yotamu anali wa zaka 25 pamene adaloŵa ufumu, ndipo adalamulira zaka 16 ku Yerusalemu. Mai wake anali Yerusa mwana wa Zadoki.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

1 Yotamu anakhala mfumu ali ndi zaka 25 ndipo analamulira mu Yerusalemu kwa zaka 16. Dzina la amayi ake linali Yerusa mwana wa Zadoki.

Onani mutuwo Koperani




2 Mbiri 27:1
9 Mawu Ofanana  

Amaziya mwana wake, Azariya mwana wake, Yotamu mwana wake,


Ndipo mfumu Uziya anali wakhate mpaka tsiku la imfa yake, nakhala m'nyumba ya padera, popeza ndiye wakhate; pakuti anadulidwa kunyumba ya Yehova; ndi Yotamu mwana wake anayang'anira nyumba ya mfumu naweruza anthu a m'dziko.


Ndipo Uziya anagona ndi makolo ake, namuika ndi makolo ake kumanda kwa mafumu; pakuti anati, Ndiye wakhate; ndi Yotamu mwana wake anakhala mfumu m'malo mwake.


Anali wa zaka makumi awiri mphambu zisanu polowa ufumu wake, nakhala mfumu mu Yerusalemu zaka khumi mphambu zisanu ndi chimodzi.


Masomphenya a Yesaya mwana wa Amozi, amene iye anaona, onena za Yuda ndi Yerusalemu, masiku a Uziya, Yotamu, Ahazi, ndi Hezekiya, mafumu a Yuda.


Mau a Yehova amene anadza kwa Hoseya mwana wa Beeri masiku a Uziya, Yotamu, Ahazi, ndi Hezekiya, mafumu a Yuda, ndi masiku a Yerobowamu mwana wa Yowasi mfumu ya Israele.


Mau a Yehova amene anadza kwa Mika wa ku Moreseti masiku a Yotamu, Ahazi, ndi Hezekiya, mafumu a Yuda, amene adaona za Samariya ndi Yerusalemu.


ndi Uziya anabala Yotamu; ndi Yotamu anabala Ahazi; ndi Ahazi anabala Hezekiya;


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa