2 Mbiri 26:9 - Buku Lopatulika9 Uziya anamanganso nsanja mu Yerusalemu pa Chipata cha Kungodya, ndi pa Chipata cha ku Chigwa, ndi popindika linga; nazilimbikitsa. Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 20149 Uziya anamanganso nsanja m'Yerusalemu pa chipata cha kungodya, ndi pa chipata cha kuchigwa, ndi popindika linga; nazilimbikitsa. Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa9 Kuwonjezera pamenepo, Uziya adamanga nsanja ku Yerusalemu ku Chipata cha ku Ndonyo, Chipata cha ku Chigwa ndi pa Mphindiko ya linga, ndipo adazilimbitsa. Onani mutuwoMawu a Mulungu mu Chichewa Chalero9 Uziya anamanga nsanja ku Yerusalemu ku Chipata Chapangodya, ku Chigwa cha Chipata ndi pokhotera mpanda, ndipo anayikamo chitetezo. Onani mutuwo |
Dziko lonse lidzasandulika, lidzanga chidikha, kuyambira ku Geba kufikira ku Rimoni, kumwera kwa Yerusalemu; ndipo pali uwupo padzakhala ponyamuka, ndipo udzakhala m'malo mwake, kuyambira ku Chipata cha Benjamini kufikira ku malo a chipata choyamba, kufikira ku Chipata cha Kungodya, ndi kuyambira Nsanja ya Hananele kufikira ku zoponderamo mphesa za mfumu.