Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




2 Mbiri 26:6 - Buku Lopatulika

6 popeza anatuluka, nayambana ndi Afilisti, nagamula linga la Gati, ndi linga la Yabine, ndi linga la Asidodi; namanga mizinda m'dziko la Asidodi, ndi mwa Afilisti.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

6 popeza anatuluka, nayambana ndi Afilisti, nagamula linga la Gati, ndi linga la Yabine, ndi linga la Asidodi; namanga midzi m'dziko la Asidodi, ndi mwa Afilisti.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

6 Nthaŵi ina Uziya adakamenyana nkhondo ndi Afilisti, nagwetsa linga la Gati ndi la Yabine ndiponso la Asidodi. Kenaka adamanga mizinda m'dziko la Asidodi ndi kwinanso m'dziko la Afilisti.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

6 Iyeyo anapita kukachita nkhondo ndi Afilisti ndipo anagwetsa makoma a Gati, Yabine ndi Asidodi. Ndipo kenaka anamanganso mizinda ya pafupi ndi Asidodi ndi malo ena pafupi ndi Afilisti.

Onani mutuwo Koperani




2 Mbiri 26:6
12 Mawu Ofanana  

Ndipo m'tsogolo mwake Davide anakantha Afilisti, nawagonjetsa Davide nalanda mudzi wa Metege Ama m'manja mwa Afilisti.


Ndipo zitatha izi, Davide anakantha Afilisti, nawagonjetsa, nalanda Gati ndi midzi yake m'manja a Afilisti.


ndi Gati, ndi Maresa, ndi Zifi,


Ndipo Yehova anautsira Yehoramu mzimu wa Afilisti, ndi wa Aarabu okhala pambali pa Akusi;


Usakondwere, iwe Filistiya, wonsewe, pothyoka ndodo inakumenya; pakuti m'muzu wa njoka mudzatuluka mphiri, ndimo chipatso chake chidzakhala njoka yamoto youluka.


Chaka chimene kazembe wa ku Asiriya anafika ku Asidodi, muja Sarigoni mfumu ya Asiriya anamtumiza iye, ndipo iye anamenyana ndi Asidodi, naugonjetsa.


ndipo ndidzalikha okhala mu Asidodi, ndi iye wogwira ndodo yachifumu mu Asikeloni; ndipo ndidzabwezera Ekeroni dzanja langa limlange; ndi Afilisti otsala adzatayika, ati Ambuye Yehova.


Pitani ku Kaline, nimuone; kuchokera komweko mupite ku Hamati wamkulu mutsikire ku Gati wa Afilisti; kodi awo ndi okoma koposa maufumu ano? Kapena malire ao aposa malire anu?


natuluka malire kunka ku mbali ya Ekeroni kumpoto; ndipo analemba malire kunka ku Sikeroni, napitirira kuphiri la Baala, natuluka ku Yabinele; ndipo matulukiro a malire anali kunyanja.


Asidodi, mizinda yake ndi midzi yake; Gaza, mizinda yake ndi midzi yake; mpaka mtsinje wa Ejipito, ndi Nyanja Yaikulu ndi malire ake.


Ndipo Afilisti anatenga likasa la Mulungu, nachoka nalo ku Ebenezeri, napita ku Asidodi.


Koma Yehova anavuta iwo a ku Asidodi ndi dzanja lake, nawaononga, nawazunza ndi mafundo, mu Asidodi ndi m'midzi yake.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa