Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




2 Mbiri 26:23 - Buku Lopatulika

23 Ndipo Uziya anagona ndi makolo ake, namuika ndi makolo ake kumanda kwa mafumu; pakuti anati, Ndiye wakhate; ndi Yotamu mwana wake anakhala mfumu m'malo mwake.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

23 Ndipo Uziya anagona ndi makolo ake, namuika ndi makolo ake kumanda kwa mafumu; pakuti anati, Ndiye wakhate; ndi Yotamu mwana wake anakhala mfumu m'malo mwake.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

23 Tsono Uziya adalondola makoko ake ndipo adamuika pamodzi ndi makolo ake ku malo a manda a mafumu, osati m'manda mwaomo, poti anthu ankati, “Iyeyu ndi wakhate.” Ndipo Yotamu mwana wake adaloŵa ufumu m'malo mwake.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

23 Uziya analondola makolo ake, ndipo anamuyika pamodzi ndi makolo ake ku malo a manda a mafumu, koma osati mʼmanda mwawomo poti anthu anati, “Iyeyu anali ndi khate.” Ndipo Yotamu mwana wake analowa ufumu mʼmalo mwake.

Onani mutuwo Koperani




2 Mbiri 26:23
7 Mawu Ofanana  

Anali wa zaka makumi atatu mphambu ziwiri polowa ufumu wake, nakhala mfumu mu Yerusalemu zaka zisanu ndi zitatu, namuka wopanda wina womlakalaka; ndipo anamuika m'mzinda wa Davide, koma si m'manda a mafumu ai.


natsutsana ndi mfumu Uziya, nati kwa iye, Sikuyenera inu, Uziya, kufukizira Yehova koma ansembe, ana a Aroni opatulidwira kufukiza; tulukani m'malo opatulika; pakuti mwalakwa; Yehova Mulungu sakulemekezanipo.


Yotamu anali wa zaka makumi awiri, mphambu zisanu polowa ufumu wake, nakhala mfumu mu Yerusalemu zaka khumi ndi zisanu ndi chimodzi; ndi dzina la make ndiye Yerusa mwana wa Zadoki.


Ndi Ahazi anagona ndi makolo ake, namuika m'mzinda wa Yerusalemu; pakuti sanadze naye kumanda a mafumu a Israele; ndipo Hezekiya mwana wake anakhala mfumu m'malo mwake.


Momwemo Manase anagona ndi makolo ake, namuika m'nyumba mwakemwake; ndi Amoni mwana wake anakhala mfumu m'malo mwake.


Chaka chimene mfumu Uziya anafa, ndinaona Ambuye atakhala pa mpando wachifumu wautali, ndi wotukulidwa, ndi zovala zake zinadzala mu Kachisi.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa