Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




2 Mbiri 26:22 - Buku Lopatulika

22 Machitidwe ena tsono a Uziya, oyamba ndi otsiriza, anawalemba Yesaya mneneri mwana wa Amozi.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

22 Machitidwe ena tsono a Uziya, oyamba ndi otsiriza, anawalemba Yesaya mneneri mwana wa Amozi.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

22 Ntchito zonse za Uziya kuyambira pa chiyambi mpaka pomaliza, adazilemba mneneri Yesaya, mwana wa Amozi.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

22 Ntchito zina za mfumu Uziya, kuyambira pachiyambi mpaka pa mapeto, zinalembedwa ndi mneneri Yesaya mwana wa Amozi.

Onani mutuwo Koperani




2 Mbiri 26:22
8 Mawu Ofanana  

Natuma Eliyakimu woyang'anira nyumbayo, ndi Sebina mlembi, ndi akulu a ansembe ofundira chiguduli, kwa Yesaya mneneri mwana wa Amozi.


Machitidwe ake tsono a Rehobowamu, zoyamba ndi zotsiriza, sizinalembedwe kodi m'buku la machitidwe a Semaya mneneriyo, ndi la Ido mlauliyo, lakunena za zibadwidwe? Ndipo panali nkhondo pakati pa Rehobowamu ndi Yerobowamu masiku onse.


Machitidwe ena tsono a Amaziya, oyamba ndi otsiriza, taonani, sanalembedwe kodi m'buku la mafumu a Yuda ndi Israele?


Ndipo Uziya anagona ndi makolo ake, namuika ndi makolo ake kumanda kwa mafumu; pakuti anati, Ndiye wakhate; ndi Yotamu mwana wake anakhala mfumu m'malo mwake.


Machitidwe ena tsono a Hezekiya, ndi ntchito zake zokoma, taonani, zilembedwa m'masomphenya a Yesaya mneneri mwana wa Amozi, ndi m'buku la mafumu a Yuda ndi Israele.


Machitidwe ena tsono a Solomoni, oyamba ndi otsiriza, sanalembedwe kodi m'buku la mau a Natani mneneri ndi m'zonenera za Ahiya wa ku Silo, ndi m'masomphenya a Ido mlauli za Yerobowamu mwana wa Nebati?


Masomphenya a Yesaya mwana wa Amozi, amene iye anaona, onena za Yuda ndi Yerusalemu, masiku a Uziya, Yotamu, Ahazi, ndi Hezekiya, mafumu a Yuda.


Chaka chimene mfumu Uziya anafa, ndinaona Ambuye atakhala pa mpando wachifumu wautali, ndi wotukulidwa, ndi zovala zake zinadzala mu Kachisi.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa