Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




2 Mbiri 26:20 - Buku Lopatulika

20 Ndipo Azariya wansembe wamkulu, ndi ansembe onse, anampenya, ndi kuona kuti anali wakhate pamphumi pake namkankhira msanga kubwalo; nafulumiranso yekha kutulukako, pakuti Yehova adamkantha.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

20 Ndipo Azariya wansembe wamkulu, ndi ansembe onse, anampenya, ndi kuona kuti anali wakhate pamphumi pake namkankhira msanga kubwalo; nafulumiranso yekha kutulukako, pakuti Yehova adamkantha.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

20 Azariya mkulu wa ansembe, pamodzi ndi ansembe onse atamuyang'ana, adangoona kuti wachita khate pa mphumi. Ansembewo adamkankhira kunja mwamsanga, ndipo iye mwini wake adatuluka msangamsanga, chifukwa chakuti Chauta adaamlanga.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

20 Azariya, mkulu wa ansembe pamodzi ndi ansembe ena onse atamuyangʼana anaona kuti anali ndi khate pamphumi pake, ndipo anamutulutsa mofulumira. Ndipo iye mwini anafulumira kutuluka, chifukwa Yehova anamulanga.

Onani mutuwo Koperani




2 Mbiri 26:20
8 Mawu Ofanana  

Koma Uziya anapsa mtima, mbale ya zofukiza ili m'dzanja lake kufukiza nayo; ndipo pakupsa mtima nao ansembe, khate linabuka pamphumi pake, pamaso pa ansembe m'nyumba ya Yehova, pambali pa guwa lofukizapo.


Ndipo mfumu Uziya anali wakhate mpaka tsiku la imfa yake, nakhala m'nyumba ya padera, popeza ndiye wakhate; pakuti anadulidwa kunyumba ya Yehova; ndi Yotamu mwana wake anayang'anira nyumba ya mfumu naweruza anthu a m'dziko.


mwana wa Abisuwa mwana wa Finehasi, mwana wa Eleazara, mwana wa Aroni wansembe wamkulu.


Ndipo Mordekai anabweranso kuchipata cha mfumu. Koma Hamani anafulumira kunka kwao, wachisoni ndi wofunda mutu wake.


ndipo wansembe aone, ndipo taonani, ngati pali chotupa choyera pakhungu, ndipo chasanduliza tsitsi likhale loyera, ndipo pachotupa pali mnofu wofiira,


Mutakafika m'dziko la Kanani, limene ndikupatsani likhale lanulanu, ndipo ndikaika nthenda yakhate m'nyumba ya dziko lanulanu;


Yehova adzakukanthani ndi nthenda yoondetsa ya chifuwa, ndi malungo, ndi chibayo, ndi kutentha thupi, ndi lupanga, chinsikwi ndi chinoni; ndipo zidzakutsatani kufikira mwatayika.


Yehova adzakukanthani ndi chilonda choipa chosachira nacho kumaondo, ndi kumiyendo, kuyambira pansi pa phazi lanu kufikira pamwamba pamutu panu.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa