Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




2 Mbiri 26:13 - Buku Lopatulika

13 Ndipo m'dzanja mwao munali khamu la nkhondo zikwi mazana atatu mphambu zikwi zisanu ndi ziwiri kudza mazana asanu ochita nkhondo ndi mphamvu yaikulu, kuthandiza mfumu alimbane ndi adani.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

13 Ndipo m'dzanja mwao munali khamu la nkhondo zikwi mazana atatu mphambu zikwi zisanu ndi ziwiri kudza mazana asanu ochita nkhondo ndi mphamvu yaikulu, kuthandiza mfumu alimbane ndi adani.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

13 Atsogoleri ameneŵa ankalamulira gulu lankhondo lokwanira asilikali 307,500, amene ankatha kumenya nkhondo mwamphamvu, kuthandiza mfumu polimbana ndi adani.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

13 Pansi pa ulamuliro wawo panali asilikali 307,500 ophunzitsidwa nkhondo, gulu lamphamvu lothandiza mfumu kulimbana ndi adani ake.

Onani mutuwo Koperani




2 Mbiri 26:13
9 Mawu Ofanana  

Ndipo atafika ku Yerusalemu Rehobowamu, anamemeza a nyumba ya Yuda ndi Benjamini amuna osankhika zikwi zana limodzi mphambu makumi asanu ndi atatu, ndiwo ankhondo, alimbane ndi Aisraele kubwezanso ufumu kwa Rehobowamu.


Ndipo kunachitika, utakhazikika ufumu wa Rehobowamu, nalimbika iye, anasiya chilamulo cha Yehova, ndi Aisraele onse pamodzi naye.


Ndipo Abiya anayambana nkhondo ali ndi khamu la ngwazi za nkhondo, amuna osankhika zikwi mazana anai; Yerobowamu atandandalitsa nkhondo yake ilimbane naye ndi amuna osankhika zikwi mazana asanu ndi atatu, ndiwo ngwazi zamphamvu.


Ndipo anati kwa Yuda, Timange mizinda iyi ndi kuizingira malinga, ndi nsanja, zitseko, ndi mipiringidzo; dziko likali pamaso pathu, popeza tafuna Yehova Mulungu wathu; tamfuna Iye, natipatsa mpumulo pozungulira ponse. Momwemo anamanga mosavutika.


Ndipo Asa anali nao ankhondo ogwira zikopa ndi mikondo, a mu Yuda zikwi mazana atatu; ndi a mu Benjamini ogwira malihawo ndi okoka mauta zikwi mazana awiri mphambu makumi asanu ndi atatu; onsewo ngwazi zamphamvu.


Ndipo Amaziya anamemeza Ayuda, nawaika monga mwa nyumba za atate ao, atsogoleri a zikwi, ndi atsogoleri a mazana, ndiwo onse a Yuda ndi Benjamini; nawawerenga a zaka makumi awiri ndi mphambu, nawapeza amuna osankhika zikwi mazana atatu akutulukira kunkhondo, ogwira mkondo ndi chikopa.


Chiwerengo chonse cha akulu a nyumba za makolo, ndiwo ngwazi zamphamvu, ndicho zikwi ziwiri mphambu mazana asanu ndi limodzi.


Ndipo Uziya anawakonzeratu ankhondo onse zikopa, ndi mikondo, ndi zisoti zachitsulo, ndi malaya achitsulo, ndi mauta, ndi miyala yoponyera.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa