Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




2 Mbiri 26:1 - Buku Lopatulika

1 Ndipo anthu onse Ayuda anatenga Uziya, ndiye wa zaka khumi mphambu zisanu ndi chimodzi, namlonga ufumu m'malo mwa atate wake Amaziya.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

1 Ndipo anthu onse Ayuda anatenga Uziya, ndiye wa zaka khumi mphambu zisanu ndi chimodzi, namlonga ufumu m'malo mwa atate wake Amaziya.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

1 Pambuyo pake anthu onse a ku Yuda adatenga Uziya, wa zaka 16, namlonga ufumu m'malo mwa Amaziya bambo wake.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

1 Kenaka anthu onse a ku Yuda anatenga Uziya amene anali wa zaka 16, namuyika kukhala mfumu mʼmalo mwa Amaziya abambo ake.

Onani mutuwo Koperani




2 Mbiri 26:1
12 Mawu Ofanana  

Chaka chachiwiri cha Yehowasi mwana wa Yehowahazi mfumu ya Israele, Amaziya mwana wa Yowasi mfumu ya Yuda analowa ufumu wake.


Ndipo anthu onse a Yuda anatenga Azariya, (ndiye Uziya), ndiye wa zaka khumi mphambu zisanu ndi chimodzi, namlonga ufumu m'malo mwa atate wake Amaziya.


Amaziya mwana wake, Azariya mwana wake, Yotamu mwana wake,


Ndipo okhala mu Yerusalemu anamlonga Ahaziya mwana wake wamng'ono akhale mfumu m'malo mwake; pakuti gulu la anthu, adadzawo pamodzi ndi Aarabu kuchigono, adapha ana oyamba onse. Momwemo Ahaziya mwana wa Yehoramu anakhala mfumu ya Yuda.


Namnyamula pa akavalo, namuika pamodzi ndi makolo ake m'mzinda wa Yuda.


Iye anamanga Eloti, naubweza kwa Yuda, mfumuyo itagona ndi makolo ake.


Koma anthu a m'dziko anapha onse adampangira chiwembu mfumu Amoni; ndi anthu a m'dziko analonga Yosiya mwana wake akhale mfumu m'malo mwake.


Masomphenya a Yesaya mwana wa Amozi, amene iye anaona, onena za Yuda ndi Yerusalemu, masiku a Uziya, Yotamu, Ahazi, ndi Hezekiya, mafumu a Yuda.


Mau a Yehova amene anadza kwa Hoseya mwana wa Beeri masiku a Uziya, Yotamu, Ahazi, ndi Hezekiya, mafumu a Yuda, ndi masiku a Yerobowamu mwana wa Yowasi mfumu ya Israele.


Mau a Amosi, amene anali mwa oweta ng'ombe a ku Tekowa, ndiwo amene anawaona za Israele masiku a Uziya mfumu ya Yuda, ndi masiku a Yerobowamu mwana wa Yowasi mfumu ya Israele, zitatsala zaka ziwiri chisanafike chivomezi.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa