Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




2 Mbiri 24:12 - Buku Lopatulika

12 Ndipo mfumu ndi Yehoyada anazipereka kwa iwo akugwira ntchito ya utumiki ya nyumba ya Yehova, nalembera amisiri omanga ndi miyala, ndi osema mitengo, akonzenso nyumba ya Yehova; ndiponso akuchita ndi chitsulo ndi mkuwa alimbitse nyumba ya Yehova.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

12 Ndipo mfumu ndi Yehoyada anazipereka kwa iwo akugwira ntchito ya utumiki ya nyumba ya Yehova, nalembera amisiri omanga ndi miyala, ndi osema mitengo, akonzenso nyumba ya Yehova; ndiponso akuchita ndi chitsulo ndi mkuwa alimbitse nyumba ya Yehova.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

12 Ndipo mfumu pamodzi ndi Yehoyada ankazipereka kwa akapitao oyang'anira ntchito ya ku Nyumba ya Chauta. Tsono adalemba amisiri omanga ndi miyala ndi amisiri a matabwa, kuti akonzenso Nyumba ya Chauta. Adalembanso amisiri ogwira ntchito ndi chitsulo ndi mkuŵa, kuti akonze Nyumba ya Chauta.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

12 Mfumu pamodzi ndi Yehoyada anapereka ndalamazo kwa anthu oyangʼanira ntchito ku Nyumba ya Yehova. Analemba ntchito amisiri a miyala ndi a matabwa kuti akonzenso Nyumba ya Yehova. Analembanso ntchito amisiri a zitsulo ndi mkuwa kuti akonze Nyumba ya Mulungu.

Onani mutuwo Koperani




2 Mbiri 24:12
7 Mawu Ofanana  

Ndipo Hiramu mfumu ya Tiro anatumiza mithenga kwa Davide ndi mitengo yamkungudza, ndi amisiri a matabwa, ndi omanga nyumba; iwo nammangira Davide nyumba.


Ndipo Solomoni anawasenzetsa akatundu anthu zikwi makumi asanu ndi awiri, ndi anthu zikwi makumi asanu ndi atatu anatema m'mapiri;


Ndipo kunali, pamene amabwera nalo bokosi alipenye mfumu, mwa manja a Alevi, nakapenya kuti ndalama zinachulukamo, amadza mlembi wa mfumu, ndi kapitao wa wansembe wamkulu, nakhuthula za m'bokosi, nalisenza ndi kubwera nalo kumalo kwake. Anatero tsiku ndi tsiku, nasonkhanitsa ndalama zochuluka.


Momwemo anachita ogwira ntchito, nikula ntchito mwa dzanja lao, nakhazikitsa iwo nyumba ya Mulungu monga mwa maonekedwe ake, nailimbitsa.


Za ana ake tsono, ndi katundu wamkulu anamsenza, ndi kumanganso kwa nyumba ya Mulungu, taonani, zilembedwa m'buku lomasulira la mafumu. Ndipo Amaziya mwana wake anakhala mfumu m'malo mwake.


Atakhala mfumu tsono zaka khumi mphambu zisanu ndi ziwiri, atayeretsa dziko ndi nyumbayi, anatuma Safani mwana wa Azaliya, ndi Maaseiya kazembe wa mzinda, ndi Yowa mwana wa Yehowahazi wolemba mbiri, akonze nyumba ya Yehova Mulungu wake.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa