2 Mbiri 24:11 - Buku Lopatulika11 Ndipo kunali, pamene amabwera nalo bokosi alipenye mfumu, mwa manja a Alevi, nakapenya kuti ndalama zinachulukamo, amadza mlembi wa mfumu, ndi kapitao wa wansembe wamkulu, nakhuthula za m'bokosi, nalisenza ndi kubwera nalo kumalo kwake. Anatero tsiku ndi tsiku, nasonkhanitsa ndalama zochuluka. Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 201411 Ndipo kunali, pamene amabwera nalo bokosi alipenye mfumu, mwa manja a Alevi, nakapenya kuti ndalama zinachulukamo, amadza mlembi wa mfumu, ndi kapitao wa wansembe wamkulu, nakhuthula za m'bokosi, nalisenza ndi kubwera nalo kumalo kwake. Anatero tsiku ndi tsiku, nasonkhanitsa ndalama zochuluka. Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa11 Nthaŵi zonse Alevi ankabwera nalo bokosilo kwa nduna zake za mfumu, akaona kuti muli ndalama zambiri. Tsono mlembi wa mfumu pamodzi ndi nduna ya mkulu wa ansembe, ankadzakhuthula ndalamazo, kenaka ankalitenga bokosilo nkulibweza pamalo pake. Umu ndimo m'mene ankachitira tsiku ndi tsiku, mwakuti adasonkha ndalama zambirimbiri. Onani mutuwoMawu a Mulungu mu Chichewa Chalero11 Nthawi ina iliyonse imene Alevi abweretsa bokosilo kwa akuluakulu a mfumu ndipo akaona kuti muli ndalama zambiri, mlembi waufumu ndi nduna yayikulu ya mkulu wa ansembe amabwera ndi kuchotsa ndalama mʼbokosi muja ndipo amalitenga kukaliyika pamalo pake. Iwo amachita izi nthawi ndi nthawi ndipo anapeza ndalama zambiri. Onani mutuwo |