Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




2 Mbiri 23:4 - Buku Lopatulika

4 Chimene muzichita ndi ichi: limodzi la magawo atatu mwa inu olowera tsiku la Sabata, la ansembe ndi Alevi, akhale olindirira pakhomo;

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

4 Chimene muzichita ndi ichi: limodzi la magawo atatu mwa inu olowera tsiku la Sabata, la ansembe ndi Alevi, akhale olindirira pakhomo;

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

4 Zimene mudzachite ndi izi: mwa inu ansembe ndi Alevi amene mukudzatumikira pa sabata, mugaŵikane patatu: gulu limodzi lidzalonde pa makomo.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

4 Tsopano zimene muti muchite ndi izi: Limodzi mwa magawo atatu a ansembe ndi Alevi amene mudzakhale pa ntchito pa Sabata muzikalondera pa khomo,

Onani mutuwo Koperani




2 Mbiri 23:4
8 Mawu Ofanana  

Nadza iwo, naitana mlonda wa mzinda, namfotokozera; ndi kuti, Tinafika ku misasa ya Aaramu, ndipo taonani, palibe munthu pomwepo, kapena mau a munthu, koma akavalo omanga, ndi abulu omanga, ndi mahema ali chimangire.


Pakuti ntchito yao ndiyo kuimirira ana a Aroni, atumikire m'nyumba ya Yehova, m'mabwalo, ndi kuzipinda, ndi kuyeretsa zopatulika zonse; inde ntchito za utumiki wa nyumba ya Mulungu;


Ndi abale ao m'midzi mwao akafikafika, atapita masiku asanu ndi awiri masabata onse, kuti akhale nao;


ndi limodzi la magawo atatu likhale kunyumba ya mfumu; ndi limodzi la magawo atatu ku Chipata cha Maziko; ndi anthu onse akhale m'mabwalo a nyumba ya Yehova.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa