Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




2 Mbiri 23:3 - Buku Lopatulika

3 Ndipo msonkhano wonse unapangana pangano ndi mfumu m'nyumba ya Mulungu. Ndipo ananena nao, Taonani, mwana wa mfumu adzakhala mfumu monga Yehova ananena za ana a Davide.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

3 Ndipo msonkhano wonse unapangana pangano ndi mfumu m'nyumba ya Mulungu. Ndipo ananena nao, Taonani, mwana wa mfumu adzakhala mfumu monga Yehova ananena za ana a Davide.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

3 Msonkhano wonsewo udachita chipangano ndi mfumu m'Nyumba ya Mulungu. Yehoyada adaŵauza anthuwo kuti, “Nayu mwana wa mfumu. Iyeyu akhale mfumu monga Chauta adanenera za ana a Davide.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

3 msonkhano wonse unachita pangano ndi mfumu mu Nyumba ya Mulungu. Yehoyada anawawuza kuti, “Mwana wa mfumu adzalamulira monga ananenera Yehova zokhudza ana a Davide.

Onani mutuwo Koperani




2 Mbiri 23:3
14 Mawu Ofanana  

Chomwecho akulu onse a Israele anadza kwa mfumu ku Hebroni; ndipo mfumu Davide anapangana nao pangano ku Hebroni pamaso pa Yehova; ndipo anamdzoza Davide mfumu ya Israele.


Pamene masiku ako akadzakwaniridwa, ndipo iwe udzagona ndi makolo ako, Ine ndidzaukitsa mbeu yako pambuyo pako, imene idzatuluka m'matumbo mwako, ndipo ndidzakhazikitsa ufumu wake.


Ndipo nyumba yako ndi ufumu wako zidzakhazikikadi ku nthawi zonse pamaso pako; mpando wachifumu wako udzakhazikika ku nthawi zonse.


kuti Yehova akakhazikitse mau ake adanenawo za ine, kuti, Ngati ana ako akasunga bwino njira zao, kuyenda moona pamaso pa Ine ndi mtima wao wonse ndi moyo wao wonse, nditi sipadzakusowa mwamuna mmodzi pa mpando wachifumu wa Israele.


pamenepo Ine ndidzakhazikitsa chimpando cha ufumu wako pa Israele nthawi yosatha, monga ndinalonjezana ndi Davide atate wako, ndi kuti, Sadzakusowa munthu wamwamuna pa mpando wachifumu wa Israele.


Ndipo Yehoyada anachita chipangano pakati pa Yehova ndi mfumu ndi anthu, akhale anthu a Yehova; pakati pa mfumunso ndi anthu.


Akulu onse omwe a Israele anadza kwa mfumu ku Hebroni; ndipo Davide anapangana nao pangano ku Hebroni pamaso pa Yehova; ndipo anamdzoza Davide akhale mfumu ya Israele monga mwa mau a Yehova, ndi dzanja la Samuele.


Koma Yehova sanafune kuononga nyumba ya Davide chifukwa cha pangano adalichita ndi Davide, ndi monga adalonjeza kumpatsa iye ndi ana ake nyali nthawi zonse.


Ndipo Yehoyada anachita pangano pakati pa iye, ndi anthu onse, ndi mfumu, kuti adzakhala anthu a Yehova.


Ndipo tsopano, Yehova Mulungu wa Israele, msungireni mtumiki wanu Davide chija mudamlonjezacho, ndi kuti, Sadzakusowa munthu pamaso panga wakukhala pa mpando wachifumu wa Israele; pokhapo ngati ana ako asamalira njira yao, kuti ayende m'chilamulo changa, monga umo unayendera iwe pamaso panga.


pamenepo ndidzakhazikitsa mpando wachifumu wa ufumu wako, monga ndinapangana ndi Davide atate wako, ndi kuti, Sadzakusowa munthu wokhala mfumu mu Israele.


Ndidzakhalitsanso mbeu yake chikhalire, ndi mpando wachifumu wake ngati masiku a m'mwamba.


Mbeu yake idzakhala kunthawi yonse, ndi mpando wachifumu wake ngati dzuwa pamaso panga.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa