Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




2 Mbiri 23:2 - Buku Lopatulika

2 Ndipo iwo anayendayenda mwa Yuda, nasonkhanitsa Alevi m'mizinda yonse ya Yuda, ndi akulu a nyumba za makolo mu Israele; nadza iwo ku Yerusalemu.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

2 Ndipo iwo anayendayenda mwa Yuda, nasonkhanitsa Alevi m'midzi yonse ya Yuda, ndi akulu a nyumba za makolo m'Israele; nadza iwo ku Yerusalemu.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

2 Iwoŵa adayendera dziko la Yuda, nasonkhanitsa Alevi onse a ku mizinda yonse ya ku Yuda ndi atsogoleri a mabanja a Aisraele, nabwera onse ku Yerusalemu.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

2 Iwo anayendayenda mʼdziko la Yuda ndipo anasonkhanitsa Alevi ndi atsogoleri a mabanja a Aisraeli ochokera mʼmizinda yonse. Atabwera ku Yerusalemu,

Onani mutuwo Koperani




2 Mbiri 23:2
7 Mawu Ofanana  

Inu ndinu akulu a nyumba za makolo a Alevi, mudzipatule inu ndi abale anu omwe, kuti mukatenge ndi kukwera nalo likasa la Yehova Mulungu wa Israele ku malo ndalikonzera.


Ndi Semaya mwana wa Netanele mlembi, ndiye wa Alevi, anawalembera pamaso pa mfumu; ndi akalonga, ndi Zadoki wansembe, ndi Ahimeleki mwana wa Abiyatara, a akulu a nyumba za makolo a ansembe ndi Alevi, anatenga nyumba imodzi ya kholo lake ya Eleazara, ndi imodzi ya Itamara.


Ndipo anali nao abale ake, ana a Yehosafati, Azariya, ndi Yehiyele, ndi Zekariya, ndi Azariya, ndi Mikaele, ndi Sefatiya, onsewa ndiwo ana a Yehosafati mfumu ya Israele.


Wodala munthu wakuchitira chifundo, nakongoletsa; adzalimbika nao mlandu wake poweruzidwa.


Taonani, Ine ndikutumizani inu monga nkhosa pakati pa mimbulu; chifukwa chake khalani ochenjera monga njoka, ndi oona mtima monga nkhunda.


Potero, penyani bwino umo muyendera, si monga opanda nzeru, koma monga anzeru;


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa