2 Mbiri 22:9 - Buku Lopatulika9 Atatero, anafunafuna Ahaziya, namgwira alikubisala mu Samariya, nabwera naye kwa Yehu, namupha; ndipo anamuika; pakuti anati, Ndiye mwana wa Yehosafati, wofuna Yehova ndi mtima wake wonse. Ndipo panalibe wina wa nyumba ya Ahaziya wa mphamvu yakusunga ufumuwo. Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 20149 Atatero, anafunafuna Ahaziya, namgwira alikubisala m'Samariya, nabwera naye kwa Yehu, namupha; ndipo anamuika; pakuti anati, Ndiye mwana wa Yehosafati, wofuna Yehova ndi mtima wake wonse. Ndipo panalibe wina wa nyumba ya Ahaziya wa mphamvu yakusunga ufumuwo. Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa9 Adafunafuna Ahaziya, ndipo adamgwira pamene ankabisala ku Samariya. Adabwera naye kwa Yehu, namupha. Anthuwo adamuika m'manda, poti ankati, “Ameneyu ndi mdzukulu wa Yehosafati uja amene ankatumikira Chauta ndi mtima wake wonse.” Choncho banja la Ahaziya linalibe munthu woti nkukhala mfumu yomalamulira. Onani mutuwoMawu a Mulungu mu Chichewa Chalero9 Kenaka anapita kukafunafuna Ahaziya, ndipo anthu ake anagwira Ahaziya pamene amabisala mu Samariya. Anabwera naye kwa Yehu ndipo anaphedwa. Iwo anamuyika mʼmanda, pakuti anati, “Iyeyu anali mwana wa Yehosafati amene anafunafuna Yehova ndi mtima wake wonse.” Kotero panalibe wamphamvu mʼbanja la Ahaziya kuti nʼkukhala mfumu. Onani mutuwo |