Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




2 Mbiri 22:7 - Buku Lopatulika

7 Kuonongeka kwa Ahaziya tsono nkwa Mulungu, kuti amuke kwa Yehoramu; pakuti atafika anatulukira pamodzi ndi Yehoramu kukayambana ndi Yehu mwana wa Nimisi, amene Yehova anamdzoza alikhe nyumba ya Ahabu.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

7 Kuonongeka kwa Ahaziya tsono nkwa Mulungu, kuti amuke kwa Yehoramu; pakuti atafika anatulukira pamodzi ndi Yehoramu kukayambana ndi Yehu mwana wa Nimisi, amene Yehova anamdzoza alikhe nyumba ya Ahabu.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

7 Koma Mulungu adazikonzeratu kuti Ahaziya aonongedwe pokacheza kwa Yoramuyo. Atafika kumeneko, adapita pamodzi ndi Yoramu kuti akakumane ndi Yehu, mwana wa Nimisi, amene Chauta adaamsankha kuti aononge banja la Ahabu.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

7 Mulungu anakonza kuti Ahaziya akaphedwe pa ulendo wake wokacheza. Ahaziya atafika, iye ndi Yoramu anapita kukakumana ndi Yehu mwana wa Nimisi, amene Yehova anamudzoza kuti akawononge banja la Ahabu.

Onani mutuwo Koperani




2 Mbiri 22:7
18 Mawu Ofanana  

Potero mfumu siinamvere anthuwo, pakuti kusintha uku kunachokera kwa Yehova, kuti akhazikitse mau ake amene Yehova ananenetsa Ahiya wa ku Silo kwa Yerobowamu mwana wa Nebati.


Yehova atero, Musamuka, ndipo musakayambana ndi abale anu ana a Israele, bwererani yense kunyumba kwake; popeza chinthuchi chachokera kwa Ine. Ndipo iwo anamvera mau a Yehova, natembenuka, nabwerera monga mwa mau a Yehova.


ukadzozenso Yehu mwana wa Nimisi akhale mfumu ya Israele; ukadzozenso Elisa mwana wa Safati wa ku Abele-Mehola akhale mneneri m'malo mwako.


Nati Yehova, Adzanyenga Ahabu ndani, kuti akwere nagwe ku Ramoti Giliyadi? Ndipo anati wina mwakuti, wina mwakuti.


Nawakantha Yehu otsala onse a nyumba ya Ahabu mu Yezireele, ndi omveka ake onse, ndi odziwana naye, ndi ansembe ake, mpaka sanatsale wa iye ndi mmodzi yense.


Nati Yoramu, Manga. Namanga galeta wake. Ndipo Yoramu mfumu ya Israele ndi Ahaziya mfumu ya Yuda anatuluka yense m'galeta wake, natuluka kukakomana ndi Yehu, nakomana naye pamunda wa Naboti mu Yezireele.


Koma pochiona ichi Ahaziya mfumu ya Yuda anathawa njira ya ku Betigahani. Namtsata Yehu, nati, Mumkanthe uyonso pagaleta; namkantha pa chikweza cha Guri chili pafupi pa Ibleamu. Nathawira iye ku Megido, namwalira komweko.


Momwemo mfumu siinamvere anthuwo; pakuti kusinthaku kudafuma kwa Mulungu, kuti Yehova akhazikitse mau ake, amene ananenetsa Ahiya wa ku Silo kwa Yerobowamu mwana wa Nebati.


Nabwerera iye kuti amchize ku Yezireele, apole mabala amene adamkantha ku Rama, pamene anayambana ndi Hazaele mfumu ya Aramu. Ndipo Ahaziya mwana wa Yehoramu mfumu ya Yuda anatsikira kukaona Yehoramu mwana wa Ahabu mu Yezireele, popeza anadwala.


Anadziwika Yehova, anachita kuweruza, woipayo anakodwa ndi ntchito ya manja ake.


Mtima wa munthu ulingalira njira yake; koma Yehova ayendetsa mapazi ake.


ndilalikira za chimaliziro kuyambira pachiyambi, ndi kuyambira nthawi zakale ndinena zinthu zimene zisanachitidwe; ndi kunena, Uphungu wanga udzakhala, ndipo ndidzachita zofuna zanga zonse;


Wanzeru ndani, kuti azindikire izi? Waluntha, kuti adziwe izi? Pakuti njira za Yehova zili zoongoka; ndipo olungama adzayendamo, koma olakwa adzagwamo.


Ndipo mudzapondereza oipa; pakuti adzakhala ngati mapulusa kumapazi anu, tsiku ndidzaikalo, ati Yehova wa makamu.


Kubwezera chilango nkwanga, kubwezera komwe, pa nyengo ya kuterereka phazi lao; pakuti tsiku la tsoka lao layandika, ndi zinthu zowakonzeratu zifulumira kudza.


Pakuti chidadzera kwa Yehova kulimbitsa mitima yao kuti athirane nao Aisraele nkhondo kuti Iye awaononge konse, kuti asawachitire chifundo koma awaononge, monga Yehova adalamulira Mose.


Koma atate wake ndi amai wake sanadziwe kuti chidachokera kwa Yehova ichi; popeza analikufuna kutola chifukwa ndi Afilisti. Ndipo nthawi ija Afilisti analamulira Israele.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa