2 Mbiri 22:6 - Buku Lopatulika6 Nabwerera iye kuti amchize ku Yezireele, apole mabala amene adamkantha ku Rama, pamene anayambana ndi Hazaele mfumu ya Aramu. Ndipo Ahaziya mwana wa Yehoramu mfumu ya Yuda anatsikira kukaona Yehoramu mwana wa Ahabu mu Yezireele, popeza anadwala. Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 20146 Nabwerera iye kuti amchize ku Yezireele, apole mabala amene adamkantha ku Rama, pamene anayambana ndi Hazaele mfumu ya Aramu. Ndipo Ahaziya mwana wa Yehoramu mfumu ya Yuda anatsikira kukaona Yehoramu mwana wa Ahabu m'Yezireele, popeza anadwala. Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa6 Tsono iye adabwerera napita ku Yezireele kuti akamchiritse mabala amene adaamlasa ku Rama, pamene ankamenyana ndi Hazaele mfumu ya ku Siriya. Motero Ahaziya mwana wa Yehoramu mfumu ya ku Yuda adapita ku Yezireele kukazonda Yoramu, mwana wa Ahabu, chifukwa chakuti ankadwala. Onani mutuwoMawu a Mulungu mu Chichewa Chalero6 kotero iye anabwerera ku Yezireeli kuti akachire mabala amene anamuvulaza ku Ramoti pa nkhondo ndi Hazaeli mfumu ya Aaramu. Ndipo Ahaziya, mwana wa Yehoramu mfumu ya Yuda anapita ku Yezireeli kukaona Yehoramu mwana wa Ahabu chifukwa anavulazidwa. Onani mutuwo |