Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




2 Mbiri 22:5 - Buku Lopatulika

5 Anayendanso m'kupangira kwao, namuka pamodzi ndi Yehoramu mwana wa Ahabu mfumu ya Israele, kukayambana nkhondo ndi Hazaele mfumu ya Aramu ku Ramoti Giliyadi; ndipo Aaramu anamlasa Yehoramu.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

5 Anayendanso m'kupangira kwao, namuka pamodzi ndi Yehoramu mwana wa Ahabu mfumu ya Israele, kukayambana nkhondo ndi Hazaele mfumu ya Aramu ku Ramoti Giliyadi; ndipo Aaramu anamlasa Yehoramu.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

5 Iyeyo adatsatanso uphungu wao, ndipo adapita pamodzi ndi Yoramu, mwana wa Ahabu mfumu ya ku Israele, kuti akamenyane nkhondo ndi Hazaele, mfumu ya ku Siriya, ku Ramoti ku Giliyadi. Kumeneko Asiriya adamlasa Yoramu.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

5 Iyeyo anatsatiranso uphungu wawo pamene anapita ndi Yehoramu, mwana wa Ahabu, mfumu ya Israeli kukachita nkhondo ndi Hazaeli mfumu ya Aramu ku Ramoti Giliyadi. Aaramu anavulaza Yehoramu,

Onani mutuwo Koperani




2 Mbiri 22:5
13 Mawu Ofanana  

Ndipo mfumu ya Israele ananena ndi anyamata ake, nati, Kodi simudziwa kuti Ramoti Giliyadi ngwathu, ndipo tangokhala chete, osaulanditsa m'dzanja la mfumu ya Aramu.


Benigebere ku Ramoti Giliyadi, iyeyo anali nayo mizinda ya Yairi mwana wa Manase ili mu Giliyadiyo, iye anali nalo dziko la Arigobu lili mu Basani, mizinda yaikulu makumi asanu ndi limodzi yamalinga ndi zitseko zamkuwa;


Ndipo Yehoramu mwana wa Ahabu analowa ufumu wa Israele mu Samariya m'chaka chakhumi mphambu zisanu ndi zitatu cha Yehosafati mfumu ya Yuda, nakhala mfumu zaka khumi ndi ziwiri.


Namuka Hazaele kukakomana naye, napita nacho chaufulu, ndicho cha zokoma zonse za mu Damasiko, zosenza ngamira makumi anai, nafika naima pamaso pake, nati, Mwana wanu Benihadadi mfumu ya Aramu, wandituma ine kwa inu, ndi kuti, Kodi ndidzachira nthenda iyi?


Ndipo Elisa mneneriyo anaitana mmodzi wa ana a aneneri, nanena naye, Udzimangire m'chuuno, nutenge nsupa iyi ya mafuta m'dzanja mwako, numuke ku Ramoti Giliyadi.


Nati Ahabu mfumu ya Israele kwa Yehosafati mfumu ya Yuda, Mupita nane kodi ku Ramoti Giliyadi? Nayankha, nati, Monga inu momwemo ine; monga anthu anu momwemo anthu anga; tidzakhala nanu ku nkhondoyi.


Ndipo kunali, pamene akapitao a magaleta anaona Yehosafati, anati, Ndiye mfumu ya Israele. Potero anamtembenukira kuyambana naye; koma Yehosafati anafuula, namthandiza Yehova; ndipo Mulungu anawapatukitsa amleke.


Natuluka Yehu mwana wa Hanani mlauli kukomana naye, nati kwa mfumu Yehosafati, Muyenera kodi kuthandiza zoipa, ndi kukonda amene adana ndi Yehova? Chifukwa cha ichi ukugwerani mkwiyo wochokera kwa Yehova.


Nabwerera iye kuti amchize ku Yezireele, apole mabala amene adamkantha ku Rama, pamene anayambana ndi Hazaele mfumu ya Aramu. Ndipo Ahaziya mwana wa Yehoramu mfumu ya Yuda anatsikira kukaona Yehoramu mwana wa Ahabu mu Yezireele, popeza anadwala.


Wodala munthuyo wosayenda mu uphungu wa oipa, kapena wosaimirira m'njira ya ochimwa, kapena wosakhala pansi pa bwalo la onyoza.


Ndipo inu mwana wake, Belisazara inu, simunadzichepetse m'mtima mwanu, chinkana munazidziwa izi zonse;


Pakuti asunga malemba a Omuri, ndi ntchito za nyumba ya Ahabu, ndipo mumayenda mu uphungu wao; kuti ndikusandulize bwinja, ndi okhalamo chotsonya; ndipo mudzasenza chitonzo cha anthu anga.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa