Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




2 Mbiri 22:4 - Buku Lopatulika

4 Ndipo anachita choipa pamaso pa Yehova, monga umo anachitira a nyumba ya Ahabu; pakuti ompangira ndi iwowa, atamwalira atate wake; ndi kuonongeka kwake nkumeneko.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

4 Ndipo anachita choipa pamaso pa Yehova, monga umo anachitira a nyumba ya Ahabu; pakuti ompangira ndi iwowa, atamwalira atate wake; ndi kuonongeka kwake nkumeneko.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

4 Adachita zoipa pamaso pa Chauta, monga momwe linkachitira banja la Ahabu. Pakuti atafa bambo wake uja, anthuwo ndiwo amene ankamupatsa uphungu pa ntchito zake zoipa.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

4 Iye anachita zoyipa pamaso pa Yehova monga momwe banja la Ahabu linachitira, pakuti atamwalira abambo ake, iwo anakhala alangizi ake, kumene kunali kudziwononga kwake.

Onani mutuwo Koperani




2 Mbiri 22:4
9 Mawu Ofanana  

Iyenso anayenda m'njira za nyumba ya Ahabu; pakuti wompangira ndi make achite choipa.


Mwananga, akakukopa ochimwa usalole.


Maganizo a olungama ndi chiweruzo; koma uphungu wa oipa unyenga.


Ukayenda ndi anzeru udzakhala wanzeru: koma mnzao wa opusa adzaphwetekedwa.


Ukangofuna, mwananga, kusochera kusiya mau akudziwitsa, leka kumva mwambo.


Ndipo mfumu Nebukadinezara inatumiza kukasonkhanitsa akalonga, akazembe, ndi ziwanga, oweruza, akulu osunga chuma, mandoda, ankhoswe, ndi olamulira onse a madera, abwere kuzulula fanoli adaliimika mfumu Nebukadinezara.


Pamenepo mfumu Nebukadinezara anadabwa, nauka msanga, nanena nati kwa mandoda ake, Kodi sitinaponye amuna atatu omangidwa m'kati mwa moto? Anayankha nati kwa mfumu, Inde mfumu.


Pakuti asunga malemba a Omuri, ndi ntchito za nyumba ya Ahabu, ndipo mumayenda mu uphungu wao; kuti ndikusandulize bwinja, ndi okhalamo chotsonya; ndipo mudzasenza chitonzo cha anthu anga.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa