Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




2 Mbiri 22:2 - Buku Lopatulika

2 Ahaziya anali wa zaka makumi anai mphambu ziwiri polowa ufumu wake, nakhala mfumu mu Yerusalemu chaka chimodzi; ndi dzina la make ndiye Ataliya mwana wa Omuri.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

2 Ahaziya anali wa zaka makumi anai mphambu ziwiri polowa ufumu wake, nakhala mfumu m'Yerusalemu chaka chimodzi; ndi dzina la make ndiye Ataliya mwana wa Omuri.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

2 Ahaziyayo anali wa zaka 42 pamene adaloŵa ufumu, ndipo adalamulira chaka chimodzi ku Yerusalemu. Mai wake anali Ataliya, mdzukulu wake wa Omuri.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

2 Ahaziya anali wa zaka 22 pamene anakhala mfumu ndipo analamulira mu Yerusalemu chaka chimodzi. Dzina la amayi ake linali Ataliya, chidzukulu cha Omuri.

Onani mutuwo Koperani




2 Mbiri 22:2
6 Mawu Ofanana  

Nagona Omuri ndi makolo ake, naikidwa mu Samariya; ndipo Ahabu mwana wake analowa ufumu m'malo mwake.


Nayenda m'njira ya mafumu a Israele, m'mene inachitira nyumba ya Ahabu; pakuti mkazi wake ndiye mwana wa Ahabu, nachita iye choipa pamaso pa Yehova.


Ahaziya ndiye wa zaka makumi awiri mphambu ziwiri polowa ufumu wake, nakhala mfumu mu Yerusalemu chaka chimodzi. Ndi dzina la make ndiye Ataliya mdzukulu wa Omuri mfumu ya Israele.


Nayenda m'njira ya mafumu a Israele, umo mwana wamkazi wa Ahabu anali mkazi wake; ndipo anachita choipa pamaso pa Yehova.


Ndipo okhala mu Yerusalemu anamlonga Ahaziya mwana wake wamng'ono akhale mfumu m'malo mwake; pakuti gulu la anthu, adadzawo pamodzi ndi Aarabu kuchigono, adapha ana oyamba onse. Momwemo Ahaziya mwana wa Yehoramu anakhala mfumu ya Yuda.


Iyenso anayenda m'njira za nyumba ya Ahabu; pakuti wompangira ndi make achite choipa.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa