2 Mbiri 22:1 - Buku Lopatulika1 Ndipo okhala mu Yerusalemu anamlonga Ahaziya mwana wake wamng'ono akhale mfumu m'malo mwake; pakuti gulu la anthu, adadzawo pamodzi ndi Aarabu kuchigono, adapha ana oyamba onse. Momwemo Ahaziya mwana wa Yehoramu anakhala mfumu ya Yuda. Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 20141 Ndipo okhala m'Yerusalemu anamlonga Ahaziya mwana wake wamng'ono akhale mfumu m'malo mwake; pakuti gulu la anthu, adadzawo pamodzi ndi Aarabu kuchigono, adapha ana oyamba onse. Momwemo Ahaziya mwana wa Yehoramu anakhala mfumu ya Yuda. Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa1 Anthu okhala mu Yerusalemu adalonga ufumu Ahaziya, mzime wa Yehoramu uja, m'malo mwa bambo wakeyo, pakuti gulu lankhondo limene lidadza pamodzi ndi Arabu kuzithandoko, linali litapha ana onse akuluakulu aamuna. Motero Ahaziya, mwana wa Yehoramu mfumu ya ku Yuda, ndiye amene adaloŵa ufumu. Onani mutuwoMawu a Mulungu mu Chichewa Chalero1 Anthu a mu Yerusalemu anayika Ahaziya mwana wamngʼono kwambiri wa Yehoramu kukhala mfumu mʼmalo mwake, popeza gulu lankhondo limene linabwera ndi Aarabu ku misasa, linapha ana onse aakulu. Motero Ahaziya mwana wa Yehoramu mfumu ya Yuda anayamba kulamulira. Onani mutuwo |