Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




2 Mbiri 21:4 - Buku Lopatulika

4 Atauka tsono Yehoramu mu ufumu wa atate wake, nadzilimbitsa, anapha ndi lupanga abale ake onse, ndi akalonga ena omwe a Israele.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

4 Atauka tsono Yehoramu m'ufumu wa atate wake, nadzilimbitsa, anapha ndi lupanga abale ake onse, ndi akalonga ena omwe a Israele.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

4 Yehoramu ataloŵa ufumu, nakhazikika pa mpando waufumu wa atate akewo, adapha abale ake onse ndi lupanga, ngakhalenso atsogoleri ena a ku Israele.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

4 Yehoramu atakhazikika pa ufumu wa abambo ake, iye anapha abale ake ndi lupanga pamodzi ndi atsogoleri ena a Israeli.

Onani mutuwo Koperani




2 Mbiri 21:4
10 Mawu Ofanana  

Kaini ndipo ananena ndi Abele mphwake. Ndipo panali pamene anali kumunda, Kaini anamuukira Abele mphwake, namupha.


Ubwere tsono, ndikupangire, kuti usunge moyo wako, ndi moyo wa mwana wako Solomoni.


koma mwayenda m'njira ya mafumu a Israele, ndi kuchititsa Yuda ndi okhala mu Yerusalemu chigololo, monga umo anachitira chigololo a nyumba ya Ahabu, mwaphanso abale anu a nyumba ya atate wanu, ndiwo abwino akuposa inu;


ndiwo anakwerera Yuda, nathyolamo, nalanda chuma chonse chinapezeka m'nyumba ya mfumu, ndi ana ake omwe, ndi akazi ake, osamsiyira mwana, koma Ahaziya yekha mwana wake wamng'ono.


Pamene Ataliya mai wake wa Ahaziya anaona kuti mwana wake adafa, anauka, naononga mbeu yonse yachifumu ya nyumba ya Yuda.


Ndipo kunali, pakulanga Yehu nyumba ya Ahabu, anapeza akalonga a Yuda, ndi ana a abale a Ahaziya, akutumikira Ahaziya, nawapha.


Kunachitika tsono, utamkhazikikira ufumu, anapha anyamata ake amene adapha mfumu atate wake.


osati monga Kaini anali wochokera mwa woipayo, namupha mbale wake. Ndipo anamupha Iye chifukwa ninji? Popeza ntchito zake zinali zoipa, ndi za mbale wake zolungama.


Ndipo anamuka kunyumba ya atate wake ku Ofura, nawapha abale ake ana a Yerubaala, ndiwo amuna makumi asanu ndi awiri, pa thanthwe limodzi; koma Yotamu mwana wamng'ono wa Yerubaala anatsalako; pakuti anabisala.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa