Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




2 Mbiri 21:2 - Buku Lopatulika

2 Ndipo anali nao abale ake, ana a Yehosafati, Azariya, ndi Yehiyele, ndi Zekariya, ndi Azariya, ndi Mikaele, ndi Sefatiya, onsewa ndiwo ana a Yehosafati mfumu ya Israele.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

2 Ndipo anali nao abale ake, ana a Yehosafati, Azariya, ndi Yehiyele, ndi Zekariya, ndi Azariya, ndi Mikaele, ndi Sefatiya, onsewa ndiwo ana a Yehosafati mfumu ya Israele.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

2 Abale ake, ana a Yehosafati, anali aŵa: Azariya, Yehiyele, Zekariya, Azariyahu, Mikaele ndi Sefatiya. Onseŵa anali ana a Yehosafati, mfumu ya ku Yuda.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

2 Abale ake a Yehoramu, ana aamuna a Yehosafati, anali Azariya, Yehieli, Zekariya, Azariyahu, Mikayeli ndi Sefatiya. Onsewa anali ana a Yehosafati mfumu ya Israeli.

Onani mutuwo Koperani




2 Mbiri 21:2
10 Mawu Ofanana  

Pamenepo akalonga a Israele ndi mfumu anadzichepetsa, nati, Yehova ali wolungama.


Atauka tsono Yehoramu mu ufumu wa atate wake, nadzilimbitsa, anapha ndi lupanga abale ake onse, ndi akalonga ena omwe a Israele.


Ndipo iwo anayendayenda mwa Yuda, nasonkhanitsa Alevi m'mizinda yonse ya Yuda, ndi akulu a nyumba za makolo mu Israele; nadza iwo ku Yerusalemu.


Ndipo anamuika m'mzinda wa Davide, pakati pa mafumu; pakuti anachita zabwino mu Israele, ndi kwa Mulungu, ndi kunyumba yake.


Nasonkhanitsa ansembe ndi Alevi, nanena nao, Mutuluke kunka kumizinda ya Yuda, ndi kusonkhanitsa kwa Aisraele onse ndalama zakukonzetsa nyumba ya Mulungu wanu chaka ndi chaka; ndipo inu fulumirani nayo ntchitoyi. Koma Alevi sanafulumire nayo.


Pakuti Yehova anachepetsa Yuda chifukwa cha Ahazi mfumu ya Israele; popeza iye anachita chomasuka pakati pa Yuda, nalakwira Yehova kwambiri.


Popeza anaphera nsembe milungu ya Damasiko yomkantha, nati, Popeza milungu ya mafumu a Aramu iwathandiza, ndiiphere nsembe, indithandize inenso. Koma inamkhumudwitsa iye, ndi Aisraele onse.


Ndi Ahazi anagona ndi makolo ake, namuika m'mzinda wa Yerusalemu; pakuti sanadze naye kumanda a mafumu a Israele; ndipo Hezekiya mwana wake anakhala mfumu m'malo mwake.


Machitidwe ena tsono a Manase, ndi pemphero lake kwa Mulungu wake, ndi mau a alauli akunena naye m'dzina la Yehova Mulungu wa Israele, taonani, zalembedwa m'machitidwe a mafumu a Israele.


Panalibe Paska wochitika mu Israele wonga ameneyu, kuyambira masiku a Samuele mneneri; panalibenso wina wa mafumu a Israele anachita Paska wotere, ngati ameneyu anachita Yosiya, ndi ansembe, ndi Alevi, ndi Ayuda onse, ndi Aisraele opezekako, ndi okhala mu Yerusalemu.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa