Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




2 Mbiri 20:9 - Buku Lopatulika

9 Chikatigwera choipa, lupanga, chiweruzo, kapena mliri, kapena njala, tidzakhala chilili pakhomo pa nyumba iyi, ndi pamaso panu, (pakuti m'nyumba muno muli dzina lanu), ndi kufuulira kwa Inu m'kusauka kwathu; ndipo mudzamvera ndi kulanditsa.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

9 Chikatigwera choipa, lupanga, chiweruzo, kapena mliri, kapena njala, tidzakhala chilili pakhomo pa nyumba iyi, ndi pamaso panu, (pakuti m'nyumba muno muli dzina lanu), ndi kufuulira kwa Inu m'kusauka kwathu; ndipo mudzamvera ndi kulanditsa.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

9 ‘Choipa chikatigwera mwachilango, monga nkhondo, mlili kapena njala, tidzaima m'Nyumba ino ndiponso pamaso panu, popeza kuti dzina lanu lili m'Nyumba muno. Tsono tidzalira kwa Inu pa mavuto athu, Inuyo mudzamva, ndipo mudzatipulumutsa.’

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

9 ‘Ngati tsoka litigwera kaya ndi lupanga lachiweruzo, kapena mliri, kapenanso njala, ife tidzayima pamaso panu patsogolo pa Nyumba ya Mulungu ino imene imatchedwa ndi Dzina lanu ndipo tidzalirira kwa inu mʼmasautso athu, ndipo Inu mudzatimvera ndi kutipulumutsa.’

Onani mutuwo Koperani




2 Mbiri 20:9
13 Mawu Ofanana  

Ndipo mverani pembedzero la kapolo wanu ndi la anthu anu Aisraele, pamene adzapemphera molunjika kumalo kuno; ndipo mverani Inu mu Mwamba mokhala Inumo; ndipo pamene mukumva, khululukirani.


Ndipo anthu anu Aisraele akawakantha adani ao chifukwa cha kuchimwira Inu, ndipo akabweranso kwa Inu, ndi kuvomereza dzina lanu, ndi kupemphera, ndi kupembedza Inu m'nyumba muno;


M'dziko mukakhala njala, mukakhala mliri, mlaza, chinoni, dzombe, kapena kapuchi, adani ao akawamangira misasa m'dziko la mizinda yao, mukakhala mliri uliwonse, kapena nthenda;


Nakhala m'mwemo iwowa, nakumangirani m'mwemo malo opatulika a dzina lanu, ndi kuti,


kuti maso anu atsegukire nyumba iyi usana ndi usiku, malo amene munanenerako kuti mudzaikako dzina lanu, kuti mumvere pemphero limene kapolo wanu adzapempha kuloza konkuno.


Kuyambira tsiku lakutulutsa Ine anthu anga m'dziko la Ejipito, sindinasankhe mzinda uliwonse m'mafuko onse a Israele, kumangamo nyumba yokhalamo dzina langa, kapena kusankha munthu aliyense akhale kalonga wa anthu anga Israele;


Pakupemphera Ezara tsono, ndi kuwulula ndi kulira misozi, ndi kudzigwetsa pansi pakhomo pa nyumba ya Mulungu, udamsonkhanira mwa Israele msonkhano waukulu ndithu wa amuna, ndi akazi, ndi ana; popeza anthu analira kulira kwakukulu.


Ndipo undiitane tsiku la chisautso, ndidzakulanditsa, ndipo iwe udzandilemekeza.


Pakuti adzakuonjola kumsampha wa msodzi, kumliri wosakaza.


Undiumbire guwa la nsembe ladothi, nundiphere pomwepo nsembe zako zopsereza, ndi nsembe zako zamtendere, nkhosa zako ndi ng'ombe zako; paliponse ndikumbukiritsa anthu dzina langa ndidzakudzera ndi kukudalitsa.


Musamalire iye, ndi kumvera mau ake; musamuwawitsa mtima, pakuti sadzakhululukira zolakwa zanu; popeza dzina langa lili m'mtima mwake.


Pakuti kumene kuli awiri kapena atatu asonkhanira m'dzina langa, ndili komweko pakati pao.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa