Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




2 Mbiri 20:8 - Buku Lopatulika

8 Nakhala m'mwemo iwowa, nakumangirani m'mwemo malo opatulika a dzina lanu, ndi kuti,

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

8 Nakhala m'mwemo iwowa, nakumangirani m'mwemo malo opatulika a dzina lanu, ndi kuti,

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

8 Mwakuti iwo atakhazikika m'dziko limenelo, adakumangirani Nyumba m'menemo, nkumati,

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

8 Iwo akhala mʼdzikolo ndipo anamangira Dzina lanu malo opatulika, nʼkumati,

Onani mutuwo Koperani




2 Mbiri 20:8
7 Mawu Ofanana  

Taonani, nditi ndilimangire dzina la Yehova Mulungu wanga nyumba, kumpatulira iyo, ndi kufukiza pamaso pake zonunkhira za fungo lokoma, ndiyo ya mkate woonekera wachikhalire, ndi ya nsembe zopsereza, m'mawa ndi madzulo, pamasabata, ndi pokhala mwezi, ndi pa zikondwerero zoikika za Yehova Mulungu wathu. Ndiwo machitidwe osatha mu Israele.


Sindinu Mulungu wathu, amene munainga nzika za m'dziko muno pamaso pa ana anu Israele, ndi kulininkha kwa mbeu ya Abrahamu bwenzi lanu kosatha?


Chikatigwera choipa, lupanga, chiweruzo, kapena mliri, kapena njala, tidzakhala chilili pakhomo pa nyumba iyi, ndi pamaso panu, (pakuti m'nyumba muno muli dzina lanu), ndi kufuulira kwa Inu m'kusauka kwathu; ndipo mudzamvera ndi kulanditsa.


Ndipo Yehova wakhazikitsa mau ake adanenawo, pakuti ndinauka ine m'malo mwa Davide atate wanga, ndipo ndikhala pa mpando wachifumu wa Israele monga analonjeza Yehova, ndipo ndamangira dzina la Yehova Mulungu wa Israele nyumbayi.


Kuyambira tsiku lakutulutsa Ine anthu anga m'dziko la Ejipito, sindinasankhe mzinda uliwonse m'mafuko onse a Israele, kumangamo nyumba yokhalamo dzina langa, kapena kusankha munthu aliyense akhale kalonga wa anthu anga Israele;


Koma ndinasankha Yerusalemu, kuti dzina langa likhale komweko; ndinasankhanso Davide akhale mfumu ya anthu anga Israele.


Motero Yehova anawapatsa Israele dziko lonse adalumbiralo kuwapatsa makolo ao: ndipo analilandira laolao, nakhala m'mwemo.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa