2 Mbiri 20:4 - Buku Lopatulika4 Namemezedwa Yuda afunsire kwa Yehova, inde anachokera kumizinda yonse ya Yuda kufuna Yehova. Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 20144 Namemezedwa Yuda afunsire kwa Yehova, inde anachokera kumidzi yonse ya Yuda kufuna Yehova. Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa4 Ayuda onse adasonkhana kuti adzapemphe chithandizo kwa Chauta. Anthu onse a ku mizinda yonse ya ku Yuda adabwera kudzapempha chithandizo kwa Chauta. Onani mutuwoMawu a Mulungu mu Chichewa Chalero4 Anthu a ku Yuda anabwera pamodzi kudzafuna thandizo kwa Yehova, ndipo anabweradi kuchokera ku mzinda uliwonse wa mu Yuda kudzafunafuna Yehova. Onani mutuwo |