Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




2 Mbiri 20:2 - Buku Lopatulika

2 Pamenepo anadza anthu akuuza Yehosafati, kuti, Ukudzerani unyinji waukulu wa anthu ochokera tsidya la nyanja ku Aramu; ndipo taonani, ali ku Hazazoni-Tamara, ndiwo Engedi.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

2 Pamenepo anadza anthu akuuza Yehosafati, kuti, Ukudzerani unyinji waukulu wa anthu ochokera tsidya la nyanja ku Aramu; ndipo taonani, ali ku Hazazoni-Tamara, ndiwo Engedi.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

2 Anthu ena adadzauza Yehosafati kuti “Chinamtindi cha anthu chikudzamenyana nanu nkhondo, kuchokera ku Edomu patsidya pa nyanja. Anthuwo ali ku Hazazoni-Tamara,” (ndiye kuti Engedi).

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

2 Anthu ena anabwera kudzamuwuza Yehosafati kuti, “Gulu lalikulu kwambiri lankhondo likubwera kudzachita nanu nkhondo lochokera ku Edomu, ku mbali ina ya Nyanja. Gululi lafika kale ku Hazazoni Tamara” (ndiye kuti Eni-Gedi).

Onani mutuwo Koperani




2 Mbiri 20:2
10 Mawu Ofanana  

Onse amenewo anadziphatikana pa chigwa cha Sidimu (pamenepo ndi pa Nyanja ya Mchere).


Ndipo anabwera nafika ku Enimisipati (kumeneko ndi ku Kadesi), nakantha dziko lonse la Aamaleke, ndiponso Aamori amene akhala mu Hazazoni-Tamara.


Wokondedwa wanga ali kwa ine ngati chipukutu cha maluwa ofiira m'minda yamipesa ya ku Engedi.


Ndipo kudzachitika, kuti asodzi adzaima komweko; kuyambira pa Engedi kufikira ku Enegilaimu kudzakhala poyanikira makoka; nsomba zao zidzakhala za mitundumitundu, ngati nsomba za mu Nyanja Yaikulu, zambirimbiri.


Ndi mbali ya kumwera kuloza kumwera ndiyo kuyambira ku Tamara kufikira ku madzi a Meribati-Kadesi, ku mtsinje wa Ejipito, ndi ku Nyanja Yaikulu. Ndiyo mbali ya kumwera kuloza kumwera.


Ndi ku malire a Gadi, mbali ya kumwera, kuloza kumwera, malire akhale kuyambira ku Tamara kufikira ku madzi a Meribati-Kadesi, ku mtsinje wa Ejipito, kufikira ku Nyanja Yaikulu.


ndi malire adzatsika ku Yordani, ndi kutuluka kwake kudzakhala ku Nyanja ya Mchere; ili ndili dziko lanu monga mwa malire ake polizinga.


ndi Nibisani, ndi Mzinda wa Mchere, ndi Engedi; mizinda isanu ndi umodzi pamodzi ndi midzi yao.


pamenepo madzi ochokera kumagwero anaima, nauka ngati mulu, kutalitu ku Adama, ndiwo mzinda wa ku mbali ya Zaretani; koma madzi akutsikira kunka ku nyanja ya chidikha, ndiyo Nyanja ya Mchere, anadulidwa konse; ndipo anthu anaoloka pandunji pa Yeriko.


Ndipo Davide anakwera kuchokera kumeneko, nakhala m'ngaka za Engedi.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa