Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




2 Mbiri 20:1 - Buku Lopatulika

1 Ndipo zitatha izi, kunachitika kuti ana a Mowabu, ndi ana a Amoni, ndi ena pamodzi ndi Aamoni, anadza kuyambana nkhondo ndi Yehosafati.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

1 Ndipo zitatha izi, kunachitika kuti ana a Mowabu, ndi ana a Amoni, ndi ena pamodzi ndi Aamoni, anadza kuyambana nkhondo ndi Yehosafati.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

1 Nthaŵi ina, Amowabu, Aamoni ndi Ameuni ena adabwera kudzamenyana nkhondo ndi Yehosafati.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

1 Zitatha izi, Amowabu ndi Aamoni pamodzi ndi Ameuni ena anabwera kudzachita nkhondo ndi Yehosafati.

Onani mutuwo Koperani




2 Mbiri 20:1
15 Mawu Ofanana  

Iwo tsono olembedwa maina anadza masiku a Hezekiya mfumu ya Yuda, nakantha mahema ao ndi zokhalamo zao, naziononga konse mpaka lero, nakhala m'malo mwao; popeza panali podyetsa zoweta zao pamenepo.


Ndipo Asa anali nao ankhondo ogwira zikopa ndi mikondo, a mu Yuda zikwi mazana atatu; ndi a mu Benjamini ogwira malihawo ndi okoka mauta zikwi mazana awiri mphambu makumi asanu ndi atatu; onsewo ngwazi zamphamvu.


Ndipo taonani, Amariya wansembe wamkulu, ndiye mkulu wanu m'milandu yonse ya Yehova; ndi Zebadiya mwana wa Ismaele, wolamulira nyumba ya Yuda, m'milandu yonse ya mfumu; ndi Alevi akhale akapitao pamaso panu. Chitani molimbika mtima, ndipo Yehova akhale ndi abwino.


Natuluka Yehu mwana wa Hanani mlauli kukomana naye, nati kwa mfumu Yehosafati, Muyenera kodi kuthandiza zoipa, ndi kukonda amene adana ndi Yehova? Chifukwa cha ichi ukugwerani mkwiyo wochokera kwa Yehova.


Naika oweruza m'dziko, m'mizinda yonse yamalinga ya mu Yuda, mzinda ndi mzinda;


Ndipo tsopano, taonani ana a Amoni, ndi Mowabu, ndi a kuphiri la Seiri, amene simunalole Israele awalowere, pakutuluka iwo m'dziko la Ejipito, koma anawapatukira osawaononga;


Ndipo Mulungu anamthandiza poyambana ndi Afilisti, ndi Aarabu okhala mu Guribaala, ndi Ameuni.


Zitatha zinthu izi zokhulupirika, anadza Senakeribu mfumu ya Asiriya, nalowera Yuda, namangira mizinda yamalinga misasa, nati adzigonjetsere iyi.


Ife tinamva kunyada kwa Mowabu, kuti iye ali wonyada ndithu; ngakhale kudzitama kwake, ndi kunyada kwake ndi mkwiyo wake; matukutuku ake ali achabe.


Ndipo panali masiku a Ahazi, mwana wa Yotamu, mwana wa Uziya, mfumu ya Yuda, kuti Rezini, mfumu ya Aramu, ndi Peka, mwana wa Remaliya, mfumu ya Israele, anakwera kunka ku Yerusalemu, kumenyana nao; koma sanathe kuupambana.


Yehova, mundilangize, koma ndi chiweruzo; si m'mkwiyo wanu, mungandithe psiti.


Za ana a Amoni. Yehova atero: Kodi Israele alibe ana aamuna? Alibe wolowa dzina? M'mwemo mfumu yao yalowa pa Gadi chifukwa chanji, ndi anthu ake akhala m'mizinda mwake?


Onse amene ndiwakonda, ndiwadzudzula ndi kuwalanga; potero chita changu, nutembenuke mtima.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa