Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




2 Mbiri 2:16 - Buku Lopatulika

16 ndipo ife tidzatema mitengo ku Lebanoni monga mwa kusowa kwanu konse; ndipo tidzabwera nayo kwa inu yoyandamitsa paphaka kufikira ku Yopa; ndipo inu mudzakwera nayo ku Yerusalemu.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

16 ndipo ife tidzatema mitengo ku Lebanoni monga mwa kusowa kwanu konse; ndipo tidzabwera nayo kwa inu yoyandamitsa paphaka kufikira ku Yopa; ndipo inu mudzakwera nayo ku Yerusalemu.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

16 Tsono ife tidzadula mtengo uliwonse wa ku Lebanoni umene mungaufune, ndipo tidzakutumizirani mitengoyo poimanga pamodzi ndi kuiyandamitsa pa nyanja mpaka ku Yopa, kuti inuyo muitenge ndi kupita nayo ku Yerusalemu.”

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

16 ndipo ife tidzadula mitengo yonse imene mukuyifuna kuchokera ku Lebanoni ndipo tidzayimanga pamodzi ndi kuyiyadamitsa pa madzi mpaka ku Yopa. Ndipo inu mudzatha kuyitenga mpaka ku Yerusalemu.”

Onani mutuwo Koperani




2 Mbiri 2:16
15 Mawu Ofanana  

Ndipo Davide anati asonkhanitse alendo okhala m'dziko la Israele; iye naika osema miyala afukule miyala, aiseme kuti amange nayo nyumba ya Mulungu.


Ndi msonkhano wonse wa Yuda, pamodzi ndi ansembe ndi Alevi, ndi msonkhano wonse wochokera kwa Israele, ndi alendo ochokera kudziko la Israele, ndi okhala mu Yuda, anakondwera.


Ndipo anthu onse otsala mwa Ahiti, ndi Aamori, ndi Aperizi, ndi Ahivi, ndi Ayebusi, osati Aisraele,


mwa ana ao otsala m'dziko pambuyo pao, amene ana a Israele sanawathe, mwa iwowa Solomoni anawachititsa thangata mpaka lero lino.


Anaperekanso ndalama kwa amisiri a miyala, ndi a mitengo; ndi chakudya, ndi chakumwa, ndi mafuta, kwa a ku Sidoni, ndi a ku Tiro, kuti atenge mikungudza ku Lebanoni, kufika nayo ku nyanja ku Yopa, monga adawalola Kirusi mfumu ya Persiya.


Koma Yona ananyamuka kuti athawire ku Tarisisi, kuzemba Yehova; ndipo anatsikira ku Yopa, napezako chombo chomuka ku Tarisisi, napereka ndalama zake, natsikira m'menemo, kuti apite nao ku Tarisisi kuzemba Yehova.


Zonse zinalengedwa ndi Iye; ndipo kopanda Iye sikunalengedwe kanthu kalikonse kolengedwa.


Chifukwa chake tumiza anthu ku Yopa, akaitane Simoni amene anenedwanso Petro; amene acherezedwa m'nyumba ya Simoni wofufuta zikopa, m'mbali mwa nyanja.


Koma mu Yopa munali wophunzira dzina lake Tabita, ndilo kunena Dorika; mkazi ameneyo anadzala ndi ntchito zabwino ndi zachifundo zimene anazichita.


Ndipo popeza Lida ndi pafupi pa Yopa, m'mene anamva ophunzirawo kuti Petro anali pomwepo, anamtumizira anthu awiri, namdandaulira, Musachedwa mudze kwa ife.


Ndipo kudadziwika ku Yopa konse: ndipo ambiri anakhulupirira Ambuye.


Ndipo kunali, kuti anakhala iye mu Yopa masiku ambiri ndi munthu Simoni wofufuta zikopa.


ndi Meyarikoni, ndi Rakoni, ndi malire pandunji pa Yopa.


Ndipo tsiku lija Yoswa anawasandutsa akutema nkhuni, ndi otungira madzi msonkhanowo, ndi guwa la nsembe la Yehova, mpaka lero lino, pamalopo akadzasankha.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa