Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




2 Mbiri 2:12 - Buku Lopatulika

12 Huramu anatinso, Alemekezedwe Yehova Mulungu wa Israele, amene analenga kumwamba ndi dziko lapansi, nampatsa mfumu Davide mwana waluso, wodziwa nzeru ndi waluntha, ammangire Yehova nyumba, ndiponso nyumba ya ufumu wake.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

12 Huramu anatinso, Alemekezedwe Yehova Mulungu wa Israele, amene analenga kumwamba ndi dziko lapansi, nampatsa mfumu Davide mwana waluso, wodziwa nzeru ndi waluntha, ammangire Yehova nyumba, ndiponso nyumba ya ufumu wake.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

12 Adatinso, “Atamandike Chauta, Mulungu wa Israele, amene adalenga kumwamba ndi dziko lapansi, amene adapatsa mfumu Davide mwana wanzeru, waluntha, ndi womvetsa zinthu bwino, woti amange nyumba ya Chauta ndiponso nyumba yaufumu ya iye mwini wake.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

12 Ndipo Hiramu anawonjezera kunena kuti, “Atamandike Yehova Mulungu wa Israeli, amene analenga kumwamba ndi dziko lapansi! Iye wamupatsa Davide mwana wanzeru, wodzaza ndi luntha ndi wozindikira, amene adzamanga Nyumba ya Mulungu ndi kudzimangira yekha nyumba yaufumu.

Onani mutuwo Koperani




2 Mbiri 2:12
21 Mawu Ofanana  

Ndipo kunachitika, pamene Hiramu anamva mau ake a Solomoni, anakondwera kwakukulu, nati, Alemekezeke Yehova lero amene wampatsa Davide mwana wanzeru akhale mfumu ya anthu aunyinji amenewa.


Ndipo Davide anati kwa khamu lonse, Mulemekeze tsono Yehova Mulungu wanu. Ndi khamu lonse linalemekeza Yehova Mulungu wa makolo ao, nawerama, nalambira Yehova, ndi mfumu.


Ndipo Solomoni anati alimangire dzina la Yehova nyumba, ndiponso nyumba ya ufumu wake.


Ndipo tsono ndatumiza munthu waluso wokhala nalo luntha, Huramuabi,


Munakhazika dziko lapansi kalelo; ndipo zakumwamba ndizo ntchito ya manja anu.


Chifukwa cha liu la kubuula kwanga mnofu wanga umamatika kumafupa anga.


Thandizo lathu lili m'dzina la Yehova, wolenga kumwamba ndi dziko lapansi.


Zakumwamba zinalengedwa ndi mau a Yehova; ndipo ndi mpweya wa m'kamwa mwake khamu lao lonse.


Koma Yehova ndiye Mulungu woona; ndiye Mulungu wamoyo, mfumu yamuyaya; pa mkwiyo wake dziko lapansi lidzanthunthumira, ndi amitundu sangapirire ukali wake.


Wolemekezeka Ambuye, Mulungu wa Israele; chifukwa Iye anayang'ana, nachitira anthu ake chiombolo.


nafuula nati, Anthuni, bwanji muchita zimenezi? Ifenso tili anthu a mkhalidwe wathu umodzimodzi ndi wanu, akulalikira kwa inu Uthenga Wabwino, wakuti musiye zinthu zachabe izi, nimutembenukire kwa Mulungu wamoyo, amene analenga zakumwamba ndi zapansi, ndi nyanja, ndi zonse zili momwemo:


Ndipo m'mene adamva, anakweza mau kwa Mulungu ndi mtima umodzi, nati, Mfumu, Inu ndinu wolenga thambo la kumwamba ndi dziko, ndi nyanja, ndi zonse zili m'menemo;


Wodalitsika Mulungu ndiye Atate wa Ambuye wathu Yesu Khristu, Iye amene, monga mwa chifundo chake chachikulu, anatibalanso ku chiyembekezo cha moyo, mwa kuuka kwa akufa kwa Yesu Khristu;


nalumbira kutchula Iye amene ali ndi moyo kunthawi za nthawi, amene analenga m'mwamba ndi zinthu zili momwemo, ndi dziko lapansi ndi zinthu zili momwemo, ndi nyanja ndi zinthu zili momwemo kuti sipadzakhalanso nthawi:


Muyenera inu, Ambuye wathu, ndi Mulungu wathu, kulandira ulemerero ndi ulemu ndi mphamvu; chifukwa mudalenga zonse, ndipo mwa chifuniro chanu zinakhala, ndipo zinalengedwa.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa