Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




2 Mbiri 19:6 - Buku Lopatulika

6 nati kwa oweruza, Khalani maso umo muchitira; pakuti simuweruzira anthu koma Yehova; ndipo ali nanu Iyeyu pakuweruza mlandu.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

6 nati kwa oweruza, Khalani maso umo muchitira; pakuti simuweruzira anthu koma Yehova; ndipo ali nanu Iyeyu pakuweruza mlandu.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

6 Tsono adauza aweruziwo kuti, “Muganize bwino zimene mukuchita, pakuti simukuweruza m'dzina la munthu ai, koma m'dzina la Chauta. Chautayo ali nanu pamene mukuweruza.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

6 Ndipo anawawuza kuti, “Muganize bwino zimene mukuchita, chifukwa simukuweruza mʼmalo mwa munthu koma Yehova, amene ali nanu pamene mukupereka chiweruzo.

Onani mutuwo Koperani




2 Mbiri 19:6
10 Mawu Ofanana  

Chenjera tsono, pakuti Yehova anakusankha iwe umange nyumba ya malo opatulika; limbika, nuchite.


Ukaona anthu alikutsendereza aumphawi, ndi kuchotsa chilungamo ndi chiweruzo mwachiwawa pa dera lina la dziko, usazizwepo; pakuti mkulu wopambana asamalira; ndipo alipo akulu ena oposa amenewo.


Musamachita chisalungamo pakuweruza mlandu; usamavomereza munthu wosauka, kapena kulemekeza munthu womveka; uweruze mlandu wa munthu mnzako molungama.


Ndipo Iye anati kwa iwo, Yang'anirani, mudzisungire kupewa msiriro uliwonse; chifukwa moyo wake wa munthu sulingana ndi kuchuluka kwa zinthu zake ali nazo.


Ndipo Iye anati, Yang'anirani musasocheretsedwe; pakuti ambiri adzadza m'dzina langa, nadzanena, Ndine amene; ndipo, Nthawi yayandikira; musawatsate pambuyo pao.


Ndipo pakumva ichi kenturiyoyo, ananka kwa kapitao wamkulu, namuuza, nanena, Nchiyani ichi uti uchite? Pakuti munthuyo ndiye Mroma.


Ndipo anati kwa iwo, Amuna inu a Israele, kadzichenjerani nokha za anthu awa, chimene muti muwachitire.


Musamasamalira munthu poweruza mlandu; ang'ono ndi akulu muwamvere chimodzimodzi; musamaopa nkhope ya munthu; popeza chiweruzo ncha Mulungu; ndipo mlandu ukakukanikani mubwere nao kwa ine, ndidzaumva.


Koma samalirani bwino kuti muchite chilangizo ndi chilamulo zimene Mose mtumiki wa Yehova anakulamulirani, kukonda Yehova Mulungu wanu, ndi kuyenda m'njira zake zonse ndi kusunga malamulo ake, ndi kumuumirira Iye, ndi kumtumikira Iye ndi mtima wanu wonse ndi moyo wanu wonse.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa