Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




2 Mbiri 19:3 - Buku Lopatulika

3 Koma zapezeka zokoma mwa inu, popeza mwazichotsa zifanizo m'dzikomo, mwalunjikitsanso mtima wanu kufuna Mulungu.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

3 Koma zapezeka zokoma mwa inu, popeza mwazichotsa zifanizo m'dzikomo, mwalunjikitsanso mtima wanu kufuna Mulungu.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

3 Komabe pali zina zabwino zimene mudachita, pakuti mudaononga mafano a m'dziko muno, ndipo mwakhala mukulimbikira ndi mtima wonse kufunafuna Mulungu.”

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

3 Komabe, muli zinthu zina zabwino mwa inu, pakuti inu mwachotsa mʼdziko muno mafano a Asera ndipo mwakhazikitsa mtima wanu pa kufunafuna Mulungu.”

Onani mutuwo Koperani




2 Mbiri 19:3
16 Mawu Ofanana  

Ndipo Aisraele onse adzamlira, nadzamuika, popeza iye yekha wa ana a Yerobowamu adzalowa m'manda; pakuti mwa iye mwapezedwa chokoma cha kwa Yehova Mulungu wa Israele m'nyumba ya Yerobowamu.


Ndipo akuwatsata iwo anadza ku Yerusalemu, ochokera m'mafuko onse a Israele, iwo akupereka mitima yao kufuna Yehova Mulungu wa Israele, kudzaphera Yehova Mulungu wa makolo ao nsembe.


Ndipo pakudzichepetsa iye mkwiyo wa Yehova unamchokera, kuti usamuononge konse; ndiponso munatsalira zokoma mu Yuda.


Koma anachita choipa, popeza sanalunjikitse mtima wake kufuna Yehova.


Nalowa chipangano chakufuna Yehova Mulungu wa makolo ao ndi mtima wao wonse, ndi moyo wao wonse;


Ndipo Yuda yense anakondwera nalo lumbirolo; pakuti adalumbira ndi mtima wao wonse, namfunafuna ndi khumbo lao lonse; ndipo anampeza; ndi Yehova anawapumulitsa pozungulirapo.


Ndipo Yehosafati anachita mantha, nalunjikitsa nkhope yake kufuna Yehova, nalalikira kusala mwa Ayuda onse.


Komatu misanje siinachotsedwe; popeza pamenepo anthu sadakonzere mitima yao kwa Mulungu wa makolo ao.


Atatero, anafunafuna Ahaziya, namgwira alikubisala mu Samariya, nabwera naye kwa Yehu, namupha; ndipo anamuika; pakuti anati, Ndiye mwana wa Yehosafati, wofuna Yehova ndi mtima wake wonse. Ndipo panalibe wina wa nyumba ya Ahaziya wa mphamvu yakusunga ufumuwo.


Momwemo Yotamu anakula mphamvu, popeza anakonza njira zake pamaso pa Yehova Mulungu wake.


wakuika mtima wake kufuna Mulungu Yehova, Mulungu wa makolo ake, chinkana sanayeretsedwe monga mwa mayeretsedwe a malo opatulika.


Pakuti Ezara adaikiratu mtima wake kuchifuna chilamulo cha Yehova, ndi kuchichita, ndi kuphunzitsa mu Israele malemba ndi maweruzo.


Mtima wanga wakhazikika, Mulungu, ndakhazika mtima; ndidzaimba, inde, ndidzaimba zolemekeza.


Pakuti ndidziwa kuti m'kati mwanga, ndiko m'thupi langa, simukhala chinthu chabwino; pakuti kufuna ndili nako, koma kuchita chabwino sindikupeza.


Ndipo Samuele analankhula ndi banja lonse la Israele nati, Ngati mukuti mubwerere kunka kwa Yehova ndi mitima yanu yonse, chotsani pakati pa inu milungu yachilendo, ndi Asitaroti, nimukonzere Yehova mitima yanu, ndi kumtumikira Iye yekha; mukatero, Iye adzakupulumutsani m'manja a Afilisti.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa