Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




2 Mbiri 18:9 - Buku Lopatulika

9 Mfumu ya Israele tsono ndi Yehosafati mfumu ya Yuda anakhala yense pa mpando wachifumu wake, ovala zovala zachifumu zao, nakhala pamalo popondera mphesa pakhomo pa chipata cha Samariya; ndi aneneri onse ananenera pamaso pao.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

9 Mfumu ya Israele tsono ndi Yehosafati mfumu ya Yuda anakhala yense pa mpando wachifumu wake, ovala zovala zachifumu zao, nakhala pamalo popondera mphesa pakhomo pa chipata cha Samariya; ndi aneneri onse ananenera pamaso pao.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

9 Nthaŵi imeneyo mfumu ya ku Israele ndi Yehosafati mfumu ya ku Yuda adaakhala pa mipando yao yaufumu, atavala zovala zao zaufumu. Pamenepo panali pa bwalo lopererapo tirigu, pa khomo la chipata cha Samariya. Ndipo aneneri onse ankalosa pamaso pa mafumuwo.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

9 Mfumu ya Israeli ndi Yehosafati mfumu ya Yuda, atavala mikanjo yawo yaufumu anali atakhala pa mipando yawo yaufumu pabwalo lopunthira tirigu pa khomo la chipata cha Samariya, pamodzi ndi aneneri onse akunenera pamaso pawo.

Onani mutuwo Koperani




2 Mbiri 18:9
12 Mawu Ofanana  

Ndipo Zedekiya mwana wa Kenana anadzisulira nyanga zachitsulo, nati, Atero Yehova, Ndi izi udzagunda Aaramu mpaka adzatha psiti.


Ndi mfumu ya Israele inati kwa Yehosafati, Ndidzadzizimbaitsa ndi kulowa kunkhondo, koma inu valani zovala zanu. Nidzizimbaitsa mfumu ya Israele, namuka iwo kunkhondo.


Pamenepo mfumu ya Israele inaitana mdindo, niti, Katenge msanga Mikaya mwana wa Imila.


Kunsi kwa manda kugwedezeka, chifukwa cha iwe, kukuchingamira podza pako; kukuutsira iwe mizimu, ngakhale onse akuluakulu a dziko lapansi; kukweza kuchokera m'mipando yao mafumu onse a amitundu.


Pamenepo akalonga onse a kunyanja adzatsika ku mipando yachifumu yao, nadzavula zovala zao zopikapika, nadzavala kunjenjemera, nadzakhala panthaka pansi, nadzanjenjemera mphindi zonse ndi kudabwa nawe.


Ndinapenyerera mpaka anaikapo mipando yachifumu, nikhalapo Nkhalamba ya kale lomwe, zovala zake zinali za mbuu ngati chipale chofewa, ndi tsitsi la pamutu pake ngati ubweya woyera, mpando wachifumu unali malawi amoto, ndi njinga zake moto woyaka.


Koma munatuluka kukaona chiyani? Munthu wovala zofewa kodi? Onani, akuvala zofewa ali m'nyumba zamafumu.


Ndipo Yesu anati kwa iwo, Indetu ndinena kwa inu, kuti inu amene munanditsata Ine, m'kubadwanso, pamene Mwana wa Munthu adzakhala pa chimpando cha ulemerero wake, inunso, mudzakhala pa mipando khumi ndi iwiri, kuweruza mafuko khumi ndi awiri a Israele.


koma ndinena kwa inu, kuti angakhale Solomoni mu ulemerero wake wonse sanavale monga limodzi la amenewa.


Ndipo Bowazi anakwera kunka kuchipata, nakhala pansi pomwepo; ndipo taona, woombolera winayo adanena Bowazi analinkupita; nati iye, Iwe uje, patuka, khala pansi apa; napatuka iye, nakhala pansi.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa