2 Mbiri 18:7 - Buku Lopatulika7 Ndipo mfumu ya Israele inati kwa Yehosafati, Atsalanso munthu mmodzi, tifunsire Yehova kwa iye; koma ndimuda, pakuti sandinenera ine kanthu kokoma, koma zoipa nthawi zonse, ndiye Mikaya mwana wa Imila. Nati Yehosafati, Isatero mfumu. Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 20147 Ndipo mfumu ya Israele inati kwa Yehosafati, Atsalanso munthu mmodzi, tifunsire Yehova kwa iye; koma ndimuda, pakuti sandinenera ine kanthu kokoma, koma zoipa nthawi zonse, ndiye Mikaya mwana wa Imila. Nati Yehosafati, Isatero mfumu. Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa7 Mfumu ya ku Israele idauza Yehosafati kuti, “Alipo wina amene angapemphe nzeru kwa Chauta, dzina lake ndi Mikaya mwana wa Imila. Koma ine ndimadana naye ameneyo popeza kuti sandilosera zabwino, nthaŵi zonse amangondilosera zoipa.” Tsono Yehosafati adati, “Iyai mfumu, musatero.” Onani mutuwoMawu a Mulungu mu Chichewa Chalero7 Mfumu ya Israeli inayankha Yehosafati kuti, “Alipo munthu mmodzi amene ife kudzera mwa iye titha kufunsira kwa Yehova, koma ndimadana naye chifukwa sandilosera zabwino koma zoyipa nthawi zonse. Iyeyu ndi Mikaya mwana wa Imula.” Yehosafati anayankha kuti, “Mfumu isanene motero.” Onani mutuwo |