2 Mbiri 18:5 - Buku Lopatulika5 Pamenepo mfumu ya Israele anamemeza aneneri aamuna mazana anai, nanena nao, Kodi timuke kunkhondo ku Ramoti Giliyadi kapena ndileke? Ndipo anati, Kweraniko, pakuti Mulungu adzaupereka m'dzanja la mfumu. Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 20145 Pamenepo mfumu ya Israele anamemeza aneneri amuna mazana anai, nanena nao, Kodi timuke kunkhondo ku Ramoti Giliyadi kapena ndileke? Ndipo anati, Kweraniko, pakuti Mulungu adzaupereka m'dzanja la mfumu. Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa5 Tsono mfumu ya ku Israele idasonkhanitsa aneneri ake 400, ndipo idaŵafunsa kuti, “Kodi ife tipite kukamenyana nkhondo ndi Ramoti-Giliyadi, kaya kapena ineyo ndileke?” Aneneriwo adamuuza kuti, “Pitani, pakuti Mulungu aupereka mzindawo kwa inu mfumu.” Onani mutuwoMawu a Mulungu mu Chichewa Chalero5 Tsono mfumu ya Israeli inasonkhanitsa aneneri 400 ndipo inawafunsa kuti, “Kodi tipite kukalimbana ndi Ramoti Giliyadi kapena tileke?” Iwo anayankha kuti, “Pitani, pakuti Mulungu adzawupereka mʼdzanja la mfumu.” Onani mutuwo |