Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




2 Mbiri 18:4 - Buku Lopatulika

4 Ndipo Yehosafati anati kwa mfumu ya Israele, Funsiranitu mau a Yehova lero lino.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

4 Ndipo Yehosafati anati kwa mfumu ya Israele, Funsiranitu mau a Yehova lero lino.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

4 Yehosafati adauza mfumu ya ku Israele kuti, “Poyamba upemphe nzeru kwa Chauta.”

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

4 Koma Yehosafati anatinso kwa mfumu ya Israeli, “Choyamba mupemphe nzeru kwa Yehova.”

Onani mutuwo Koperani




2 Mbiri 18:4
13 Mawu Ofanana  

Ndipo zitatha izi Davide anafunsira kwa Yehova nati, Kodi ndikwere kunka m'mizinda wina wa Yuda? Ndipo Yehova ananena naye, Kwera. Davide nanena naye, Ndikwere kuti? Ndipo anati, Ku Hebroni.


Ndipo Davide anafunsira kwa Yehova nati, Kodi ndimuke kuyambana nao Afilistiwo? Mudzawapereka m'dzanja langa kodi? Ndipo Yehova ananena ndi Davide, Pita, pakuti zoonadi ndidzapereka Afilisti m'dzanja lako.


Ndipo pamene Davide anafunsira kwa Yehova, Iye anati, Usamuke, koma ukawazungulire kumbuyo kuti ukawatulukire pandunji pa mkandankhuku.


Nati Ahabu mfumu ya Israele kwa Yehosafati mfumu ya Yuda, Mupita nane kodi ku Ramoti Giliyadi? Nayankha, nati, Monga inu momwemo ine; monga anthu anu momwemo anthu anga; tidzakhala nanu ku nkhondoyi.


Pamenepo mfumu ya Israele anamemeza aneneri aamuna mazana anai, nanena nao, Kodi timuke kunkhondo ku Ramoti Giliyadi kapena ndileke? Ndipo anati, Kweraniko, pakuti Mulungu adzaupereka m'dzanja la mfumu.


Koma kwa mfumu ya Yuda amene anakutumizani kufunsira kwa Yehova, muzitero kwa iye, Atero Yehova Mulungu wa Israele, Kunena za mau udawamva,


Chinthu chimodzi ndinachipempha kwa Yehova, ndidzachilondola ichi, Kuti ndikhalitse m'nyumba ya Yehova masiku onse a moyo wanga, kupenya kukongola kwake kwa Yehova ndi kufunsitsa mu Kachisi wake.


Tifunsirenitu ife kwa Yehova; pakuti Nebukadinezara mfumu wa ku Babiloni atithira ife nkhondo; kapena Yehova adzatichitira ife monga mwa ntchito zake zolapitsa, kuti atichokere.


Wobadwa ndi munthu iwe lankhula ndi akulu a Israele, nunene nao, Atero Ambuye Yehova, Mwadza kodi kufunsira kwa Ine? Pali Ine, sindidzafunsidwa ndi inu, ati Ambuye Yehova.


Chifukwa chake Davide anafunsira kwa Yehova, nati, Ndimuke kodi kukakantha Afilisti aja? Ndipo Yehova anati kwa Davide, Muka, nukanthe Afilisti, ndi kupulumutsa Keila.


Tsono Davide anafunsiranso kwa Yehova. Ndipo Yehova anamyankha iye, nati, Nyamuka, nutsikire ku Keila; pakuti ndidzapereka Afilisti m'dzanja lako.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa