Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




2 Mbiri 18:3 - Buku Lopatulika

3 Nati Ahabu mfumu ya Israele kwa Yehosafati mfumu ya Yuda, Mupita nane kodi ku Ramoti Giliyadi? Nayankha, nati, Monga inu momwemo ine; monga anthu anu momwemo anthu anga; tidzakhala nanu ku nkhondoyi.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

3 Nati Ahabu mfumu ya Israele kwa Yehosafati mfumu ya Yuda, Mupita nane kodi ku Ramoti Giliyadi? Nayankha, nati, Monga inu momwemo ine; monga anthu anu momwemo anthu anga; tidzakhala nanu ku nkhondoyi.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

3 Ndiye Ahabu mfumu ya ku Israele adafunsa Yehosafati mfumu ya ku Yuda kuti, “Kodi udzapita nane limodzi ku Ramoti-Giliyadi?” Iyeyo adayankha kuti, “Ine ndili nanu limodzi, anthu anga nganu. Ifeyo tidzakhala nanu pa nkhondo.”

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

3 Ahabu mfumu ya Israeli anafunsa Yehosafati mfumu ya Yuda kuti, “Kodi mudzapita nane kukalimbana ndi Ramoti Giliyadi?” Yehosafati anayankha kuti, “Ine ndili ngati inu nomwe, ndi anthu anga ngati anthu anu. Ife tikhala nanu limodzi pa nkhondoyi.”

Onani mutuwo Koperani




2 Mbiri 18:3
9 Mawu Ofanana  

Tsono anati kwa Yehosafati, Kodi udzapita nane kunkhondo ku Ramoti Giliyadi? Ndipo Yehosafati anati kwa mfumu ya Israele, M'mene ukhalira iwe ndi momwe ndikhalira ndine; anthu anga monga anthu ako, akavalo anga monga akavalo ako.


Benigebere ku Ramoti Giliyadi, iyeyo anali nayo mizinda ya Yairi mwana wa Manase ili mu Giliyadiyo, iye anali nalo dziko la Arigobu lili mu Basani, mizinda yaikulu makumi asanu ndi limodzi yamalinga ndi zitseko zamkuwa;


Nakatumiza mau kwa Yehosafati mfumu ya Yuda, ndi kuti, Mfumu ya Mowabu wapandukana ndi ine; kodi udzamuka nane kukathira nkhondo pa Mowabu? Nati, Ndidzakwera: ine ndikhala ngati iwe, anthu anga ngati anthu ako, akavalo anga ngati akavalo ako.


Ndipo zitatha zaka zina, anatsikira kwa Ahabu ku Samariya. Ndi Ahabu anamphera iye ndi anthu anali naye nkhosa, ndi ng'ombe zochuluka; namnyenga akwere naye pamodzi ku Ramoti Giliyadi.


Ndipo Yehosafati anati kwa mfumu ya Israele, Funsiranitu mau a Yehova lero lino.


Natuluka Yehu mwana wa Hanani mlauli kukomana naye, nati kwa mfumu Yehosafati, Muyenera kodi kuthandiza zoipa, ndi kukonda amene adana ndi Yehova? Chifukwa cha ichi ukugwerani mkwiyo wochokera kwa Yehova.


Kodi sindidana nao iwo akudana ndi Inu, Yehova? Ndipo kodi sindimva nao chisoni iwo akuukira Inu?


ndipo musayanjane nazo ntchito za mdima zosabala kanthu, koma makamakanso muzitsutse;


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa