Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




2 Mbiri 18:2 - Buku Lopatulika

2 Ndipo zitatha zaka zina, anatsikira kwa Ahabu ku Samariya. Ndi Ahabu anamphera iye ndi anthu anali naye nkhosa, ndi ng'ombe zochuluka; namnyenga akwere naye pamodzi ku Ramoti Giliyadi.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

2 Ndipo zitatha zaka zina, anatsikira kwa Ahabu ku Samariya. Ndi Ahabu anamphera iye ndi anthu anali naye nkhosa, ndi ng'ombe zochuluka; namnyenga akwere naye pamodzi ku Ramoti Giliyadi.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

2 Patapita zaka zina, Yehosafatiyo adapita kwa Ahabu ku Samariya. Ahabuyo adapha nkhosa ndi ng'ombe zambirimbiri kuphera Yehosafatiyo ndi anthu amene anali naye, pofuna kumkopa kuti akalimbane ndi Ramoti-Giliyadi.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

2 Patapita zaka zina, iye anapita kukacheza kwa Ahabu mu Samariya. Ahabu anaphera iye pamodzi ndi anthu amene anali naye, nkhosa zambiri ndi ngʼombe ndipo anamuwumiriza kuti akathire nawo nkhondo Ramoti Giliyadi

Onani mutuwo Koperani




2 Mbiri 18:2
12 Mawu Ofanana  

Ndipo Adoniya anapha nkhosa ndi ng'ombe ndi nyama zonona pamwala pa Zoheleti, uli pafupi ndi chitsime cha Rogele, naitana abale ake onse ana a mfumu, ndi anthu onse a Yuda anyamata a mfumu;


Ndipo kunachitika, atapita masiku ena mtsinje udaphwa, popeza munalibe mvula m'dziko.


Benigebere ku Ramoti Giliyadi, iyeyo anali nayo mizinda ya Yairi mwana wa Manase ili mu Giliyadiyo, iye anali nalo dziko la Arigobu lili mu Basani, mizinda yaikulu makumi asanu ndi limodzi yamalinga ndi zitseko zamkuwa;


Ndipo Elisa mneneriyo anaitana mmodzi wa ana a aneneri, nanena naye, Udzimangire m'chuuno, nutenge nsupa iyi ya mafuta m'dzanja mwako, numuke ku Ramoti Giliyadi.


Nati Ahabu mfumu ya Israele kwa Yehosafati mfumu ya Yuda, Mupita nane kodi ku Ramoti Giliyadi? Nayankha, nati, Monga inu momwemo ine; monga anthu anu momwemo anthu anga; tidzakhala nanu ku nkhondoyi.


Natuluka Yehu mwana wa Hanani mlauli kukomana naye, nati kwa mfumu Yehosafati, Muyenera kodi kuthandiza zoipa, ndi kukonda amene adana ndi Yehova? Chifukwa cha ichi ukugwerani mkwiyo wochokera kwa Yehova.


Koma pochitika ichi chonse sindinkakhale ku Yerusalemu; pakuti chaka cha makumi atatu ndi chachiwiri cha Arita-kisereksesi mfumu ya Babiloni ndinafika kwa mfumu, ndipo atapita masiku ena ndinapempha mfumu indilole;


ndiyo Bezeri, m'chipululu, m'dziko lachidikha, ndiwo wa Arubeni; ndi Ramoti mu Giliyadi, ndiwo wa Agadi; ndi Golani, mu Basani, ndiwo wa Amanase.


Ndipo tsidya lija la Yordani kum'mawa kwa Yeriko, anaika Bezeri m'chipululu, kuchidikha, wa fuko la Rubeni, ndi Ramoti mu Giliyadi wa fuko la Gadi, ndi Golani mu Basani wa fuko la Manase.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa