Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




2 Mbiri 18:12 - Buku Lopatulika

12 Ndipo mthenga wakukaitana Mikaya ananena naye, ndi kuti, Taonani, mau a aneneri anenera mfumu chokoma ngati m'kamwa mmodzi; mau anu tsono akhaletu ngati amodzi a iwowa, nimunene chokoma.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

12 Ndipo mthenga wakukaitana Mikaya ananena naye, ndi kuti, Taonani, mau a aneneri anenera mfumu chokoma ngati m'kamwa mmodzi; mau anu tsono akhaletu ngati amodzi a iwowa, nimunene chokoma.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

12 Wamthenga uja amene adaapita kukaitana Mikaya, adamuuza Mikayayo kuti, “Onani, mau onse amene akunena aneneri, akulosera mfumu zabwino. Ndiye nanunso mau anu akhale ofanafana ndi mau awo. Muzilosa zabwino.”

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

12 Wauthenga amene anapita kukayitana Mikaya anati kwa iye, “Taonani aneneri ena onse ngati munthu mmodzi akulosera za chipambano cha mfumu. Mawu anunso agwirizane ndi awo ndipo muyankhule zabwino.”

Onani mutuwo Koperani




2 Mbiri 18:12
11 Mawu Ofanana  

Ndi aneneri onse ananenera momwemo, ndi kuti, Kwerani ku Ramoti Giliyadi, mudzapindulako; pakuti Yehova adzaupereka m'dzanja la mfumu.


Nati Mikaya, Pali Yehova, chonena Mulungu wanga ndidzanena chomwechi.


Ndipo ukuti, Adziwa chiyani Mulungu? Aweruza kodi mwa mdima wa bii?


Anena m'mtima mwake, Mulungu waiwala; wabisa nkhope yake; sapenya nthawi zonse.


amene amati kwa alauli, Mtima wanu usapenye; ndi kwa aneneri, Musanenere kwa ife zinthu zoona, munene kwa ife zinthu zamyadi, munenere zonyenga;


Akondweretsa mfumu ndi zoipa zao, ndi akalonga ndi mabodza ao.


koma usaneneranso ku Betele; pakuti pamenepo mpamalo opatulika a mfumu, ndiyo nyumba yachifumu.


Munthu akayenda ndi mtima wachinyengo ndi kunama, ndi kuti, Ndidzanenera kwa iwe za vinyo ndi chakumwa chakuledzeretsa; iye ndiye mneneri wa anthu ake.


Musamanenera, amanenera ati. Sadzanenera kwa awa; matonzo sadzachoka.


anasonkhana kuponyana ndi Yoswa ndi Israele, ndi mtima umodzi.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa