Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




2 Mbiri 18:11 - Buku Lopatulika

11 Ndi aneneri onse ananenera momwemo, ndi kuti, Kwerani ku Ramoti Giliyadi, mudzapindulako; pakuti Yehova adzaupereka m'dzanja la mfumu.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

11 Ndi aneneri onse ananenera momwemo, ndi kuti, Kwerani ku Ramoti Giliyadi, mudzapindulako; pakuti Yehova adzaupereka m'dzanja la mfumu.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

11 Aneneri onsewo adalosa chimodzimodzi, adati, “Pitani ku Ramoti-Giliyadi, ndipo mukapambana. Chauta aupereka mzindawo kwa inu mfumu.”

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

11 Aneneri ena onse amanenera chimodzimodzi kuti, “Kathireni nkhondo Ramoti Giliyadi ndipo kapambaneni, pakuti Mulungu adzamupereka mʼdzanja la mfumu.”

Onani mutuwo Koperani




2 Mbiri 18:11
11 Mawu Ofanana  

Benigebere ku Ramoti Giliyadi, iyeyo anali nayo mizinda ya Yairi mwana wa Manase ili mu Giliyadiyo, iye anali nalo dziko la Arigobu lili mu Basani, mizinda yaikulu makumi asanu ndi limodzi yamalinga ndi zitseko zamkuwa;


Ndipo Zedekiya mwana wa Kenana anadzisulira nyanga zachitsulo, nati, Atero Yehova, Ndi izi udzagunda Aaramu mpaka adzatha psiti.


Ndipo mthenga wakukaitana Mikaya ananena naye, ndi kuti, Taonani, mau a aneneri anenera mfumu chokoma ngati m'kamwa mmodzi; mau anu tsono akhaletu ngati amodzi a iwowa, nimunene chokoma.


Pamenepo mfumu ya Israele anamemeza aneneri aamuna mazana anai, nanena nao, Kodi timuke kunkhondo ku Ramoti Giliyadi kapena ndileke? Ndipo anati, Kweraniko, pakuti Mulungu adzaupereka m'dzanja la mfumu.


Atero Yehova za aneneri akulakwitsa anthu anga; akuluma ndi mano ao, ndi kufuula, Mtendere; ndipo aliyense wosapereka m'kamwa mwao, amkonzera nkhondo;


Amenewo ndiwo odandaula, oderera, akuyenda monga mwa zilakolako zao (ndipo pakamwa pao alankhula zazikuluzikulu), akutama anthu chifukwa cha kupindula nako.


Ndipo chinagwidwa chilombocho, ndi pamodzi nacho mneneri wonyenga amene adachita zizindikiro pamaso pake, zimene anasokeretsa nazo iwo amene adalandira lemba la chilombo, ndi iwo akulambira fano lake; iwo awiri anaponyedwa ali moyo m'nyanja yamoto yakutentha ndi sulufure:


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa