Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




2 Mbiri 18:10 - Buku Lopatulika

10 Ndipo Zedekiya mwana wa Kenana anadzisulira nyanga zachitsulo, nati, Atero Yehova, Ndi izi udzagunda Aaramu mpaka adzatha psiti.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

10 Ndipo Zedekiya mwana wa Kenana anadzisulira nyanga zachitsulo, nati, Atero Yehova, Ndi izi udzagunda Aaramu mpaka adatha psiti.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

10 Wina mwa iwo, Zedeki, mwana wa Kenana, adaadzisulira nyanga zachitsulo. Iyeyo adati, “Chauta akunena kuti, ‘Ndi nyangazi udzamegonjetsa Asiriya ndi kuŵaonongeratu.’ ”

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

10 Tsono Zedekiya mwana wa Kenaana anapanga nyanga zachitsulo ndipo analengeza kuti, “Yehova akuti, ‘Ndi nyanga izi udzagunda Aaramu mpaka atawonongedwa!’ ”

Onani mutuwo Koperani




2 Mbiri 18:10
15 Mawu Ofanana  

Ndipo Zedekiya mwana wa Kenana anadzisulira nyanga zachitsulo, nati, Atero Yehova, Ndi izi mudzagunda nazo Aaramu mpaka atatha psiti.


Ndi aneneri onse ananenera momwemo, ndi kuti, Kwerani ku Ramoti Giliyadi, mudzapindulako; pakuti Yehova adzaupereka m'dzanja la mfumu.


Mfumu ya Israele tsono ndi Yehosafati mfumu ya Yuda anakhala yense pa mpando wachifumu wake, ovala zovala zachifumu zao, nakhala pamalo popondera mphesa pakhomo pa chipata cha Samariya; ndi aneneri onse ananenera pamaso pao.


Anena chinenere kwa iwo akundinyoza Ine, ati Yehova, Mudzakhala ndi mtendere; ndipo kwa yense amene ayenda m'kuumirira kwa mtima wake amati, Palibe choipa chidzagwera inu.


Sindinatuma aneneri awa, koma anathamanga; sindinanene ndi iwo, koma ananenera.


Ndamva chonena aneneri, amene anenera zonama m'dzina langa, kuti, Ndalota, ndalota.


Taonani, Ine ndidana ndi aneneri, ati Yehova, amene achita ndi malilime ao, ndi kuti, Ati Iye.


Yehova atero kwa ine: Udzipangire zomangira ndi magoli, nuziike pakhosi pako;


Atero Yehova wa makamu, Mulungu wa Israele, za Ahabu mwana wake wa Koliya, ndi za Zedekiya mwana wake wa Maaseiya, amene anenera zonama m'dzina langa: Taonani, Ndidzawapereka m'dzanja la Nebukadinezara mfumu ya ku Babiloni; ndipo iye adzawapha pamaso panu;


Simunaona masomphenya opanda pake kodi? Simunanena ula wabodza kodi? Pakunena inu, Atero Yehova; chinkana sindinanene?


Ndipo aneneri ao anawamatira ndi dothi losapondeka, ndi kuonera zopanda pake, ndi kuwaombezera mabodza, ndi kuti, Atero Ambuye Yehova, posanena Yehova.


Ndipo monga momwe Yane ndi Yambere anatsutsana naye Mose, kotero iwonso atsutsana nacho choonadi; ndiwo anthu ovunditsitsa mtima, osatsimikizidwa pachikhulupiriro.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa