Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




2 Mbiri 18:1 - Buku Lopatulika

1 Yehosafati tsono anali nacho chuma ndi ulemu zomchulukira, nachita chibale ndi Ahabu.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

1 Yehosafati tsono anali nacho chuma ndi ulemu zomchulukira, nachita chibale ndi Ahabu.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

1 Yehosafati anali ndi chuma chambiri ndi ulemerero waukulu. Tsono adachita chigwirizano chaukwati ndi banja la Ahabu.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

1 Tsono Yehosafati anali ndi chuma chambiri ndi ulemu, ndipo iye anachita mgwirizano wa ukwati ndi Ahabu.

Onani mutuwo Koperani




2 Mbiri 18:1
17 Mawu Ofanana  

Koma panalibe wina ngati Ahabu wakudzigulitsa kuchita choipa pamaso pa Yehova, amene Yezebele mkazi wake anamfulumiza.


Ndipo Aaramu ndi Aisraele anakhala chete zaka zitatu, osathirana nkhondo.


Tsono machitidwe ena a Yehosafati, ndi mphamvu anaionetsayo, ndi umo anathira nkhondo, sizinalembedwe kodi m'buku la machitidwe a mafumu a Yuda?


Pamene Ataliya make wa Ahaziya anaona kuti mwana wake wafa, ananyamuka, naononga mbeu yonse yachifumu.


Nayenda m'njira ya mafumu a Israele, m'mene inachitira nyumba ya Ahabu; pakuti mkazi wake ndiye mwana wa Ahabu, nachita iye choipa pamaso pa Yehova.


Ndipo Yehosafati anakula chikulire, namanga mu Yuda nyumba zansanja, ndi mizinda ya chuma.


Chifukwa chake Yehova anakhazikitsa ufumuwo m'dzanja lake, ndi onse Ayuda anabwera nayo mitulo kwa Yehosafati; ndipo zidamchulukira chuma ndi ulemu.


Ndipo kunali, pamene akapitao a magaleta anaona Yehosafati, anati, Ndiye mfumu ya Israele. Potero anamtembenukira kuyambana naye; koma Yehosafati anafuula, namthandiza Yehova; ndipo Mulungu anawapatukitsa amleke.


Natuluka Yehu mwana wa Hanani mlauli kukomana naye, nati kwa mfumu Yehosafati, Muyenera kodi kuthandiza zoipa, ndi kukonda amene adana ndi Yehova? Chifukwa cha ichi ukugwerani mkwiyo wochokera kwa Yehova.


Zitatha izi, Yehosafati mfumu ya Yuda anaphatikana ndi Ahaziya mfumu ya Israele, yemweyo anachita moipitsitsa;


Nayenda m'njira ya mafumu a Israele, umo mwana wamkazi wa Ahabu anali mkazi wake; ndipo anachita choipa pamaso pa Yehova.


Koma muyambe mwafuna Ufumu wake ndi chilungamo chake, ndipo zonse zimenezo zidzaonjezedwa kwa inu.


Musakhale omangidwa m'goli ndi osakhulupirira osiyana; pakuti chilungamo chigawana bwanji ndi chosalungama? Kapena kuunika kuyanjana bwanji ndi mdima?


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa