Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




2 Mbiri 17:9 - Buku Lopatulika

9 Ndipo anaphunzitsa mu Yuda ali nalo buku la chilamulo la Yehova, nayendayenda m'mizinda yonse ya Yuda, naphunzitsa mwa anthu.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

9 Ndipo anaphunzitsa m'Yuda ali nalo buku la chilamulo la Yehova, nayendayenda m'midzi yonse ya Yuda, naphunzitsa mwa anthu.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

9 Ankaphunzitsa ku Yuda, ali ndi buku la malamulo a Chauta. Ndipo adayendera mizinda yonse ya ku Yuda, namaphunzitsa pakati pa anthu.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

9 Iwo anaphunzitsa mu Yuda monse atatenga Buku la Malamulo a Yehova iwo anayenda mʼmizinda yonse ya ku Yuda ndipo anaphunzitsa anthu.

Onani mutuwo Koperani




2 Mbiri 17:9
22 Mawu Ofanana  

Masiku ambiri tsono Israele anakhala wopanda Mulungu woonayo, ndi wopanda wansembe wakuphunzitsa, ndi wopanda chilamulo;


Yehosafati anaikanso mu Yerusalemu Alevi, ndi ansembe ena, ndi akulu a nyumba za makolo mu Israele, aweruzire Yehova, nanena milandu. Ndipo anabwerera kudza ku Yerusalemu.


Nati kwa Alevi akuphunzitsa Aisraele onse, ndiwo opatulikira Yehova, Ikani likasa lopatulika m'nyumba imene Solomoni mwana wa Davide mfumu ya Israele anaimanga; silikhalanso katundu pa mapewa anu; tsopano mutumikire Yehova Mulungu wanu, ndi anthu ake Israele.


Ndi Yesuwa, ndi Bani, ndi Serebiya, Yamini, Akubu, Sabetai, Hodiya, Maaseiya, Kelita, Azariya, Yozabadi, Hanani, Pelaya, ndi Alevi, anadziwitsa anthu chilamulocho; ndi anthu anali chilili pamalo pao.


Kuchilamulo ndi kuumboni! Ngati iwo sanena malinga ndi mau awa, ndithu sadzaona mbandakucha.


Pakuti milomo ya wansembe iyenera kusunga chidziwitso, ndi anthu ayenera kufunafuna chilamulo pakamwa pake; pakuti iye ndiye mthenga wa Yehova wa makamu.


Koma pamene angakuzunzeni inu m'mudzi uwu, thawirani mwina: indetu ndinena kwa inu, Simudzaitha mizinda ya Israele, kufikira Mwana wa Munthu atadza.


Ndipo panali, pamene Yesu anatha kuwafotokozera ophunzira ake khumi ndi awiri, Iye anachokera kumeneko kukaphunzitsa ndi kulalikira m'mizinda mwao.


Musanthula m'malembo, popeza muyesa kuti momwemo muli nao moyo wosatha; ndipo akundichitira Ine umboni ndi iwo omwewo;


Pakuti mukadakhulupirira Mose, mukadakhulupirira Ine; pakuti iyeyu analembera za Ine.


Ndipo m'mene adatha kuwerenga chilamulo ndi aneneri, akulu a sunagoge anatuma wina kwa iwo, ndi kunena, Amuna inu, abale, ngati muli nao mau akudandaulira anthu, nenani.


Pakuti Mose, kuyambira pa mibadwo yakale ali nao m'mizinda yonse amene amlalikira, akuwerenga mau ake m'masunagoge masabata onse.


Ndipo pamene adampangira tsiku, anadza kunyumba yake anthu ambiri; amenewo anawafotokozera, ndi kuchitira umboni Ufumu wa Mulungu, ndi kuwakopa za Yesu, zochokera m'chilamulo cha Mose ndi mwa aneneri, kuyambira mamawa kufikira madzulo.


Koma Filipo anapezedwa ku Azoto; ndipo popitapita analalikira Uthenga Wabwino m'midzi yonse, kufikira anadza iye ku Kesareya.


Zambiri monsemonse: choyamba, kuti mau a Mulungu anaperekedwa kwa iwo.


akalankhula wina, alankhule ngati manenedwe a Mulungu; wina akatumikira, achite ngati mu mphamvu imene Mulungu ampatsa, kuti m'zonse Mulungu alemekezedwe mwa Yesu Khristu, amene ali nao ulemerero ndi mphamvu kunthawi za nthawi. Amen.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa