Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




2 Mbiri 17:7 - Buku Lopatulika

7 Chaka chachitatu cha ufumu wake anatuma akalonga ake, ndiwo Benihayili, ndi Obadiya, ndi Zekariya, ndi Netanele, ndi Mikaya, aphunzitse m'mizinda ya Yuda;

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

7 Chaka chachitatu cha ufumu wake anatuma akalonga ake, ndiwo Benihayili, ndi Obadiya, ndi Zekariya, ndi Netanele, ndi Mikaya, aphunzitse m'midzi ya Yuda;

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

7 Pa chaka chachitatu cha ufumu wake, Yehosafati adatuma nduna zake, Benihali, Obadiya, Zekariya, Netanele ndi Mikaya, kuti akaphunzitse ku mizinda ya ku Yuda.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

7 Mʼchaka chachitatu cha ufumu wake, iye anatuma akuluakulu ake Beni-Haili, Obadiya, Zekariya, Netaneli ndi Mikaya kukaphunzitsa mʼmizinda ya Yuda.

Onani mutuwo Koperani




2 Mbiri 17:7
20 Mawu Ofanana  

Masiku ambiri tsono Israele anakhala wopanda Mulungu woonayo, ndi wopanda wansembe wakuphunzitsa, ndi wopanda chilamulo;


Ndipo Hezekiya ananena motonthoza mtima kwa Alevi onse akuzindikira bwino za utumiki wa Yehova. Ndipo anadya pamkomano masiku asanu ndi awiri, naphera nsembe zoyamika, ndi kulemekeza Yehova Mulungu wa makolo ao.


Nati kwa Alevi akuphunzitsa Aisraele onse, ndiwo opatulikira Yehova, Ikani likasa lopatulika m'nyumba imene Solomoni mwana wa Davide mfumu ya Israele anaimanga; silikhalanso katundu pa mapewa anu; tsopano mutumikire Yehova Mulungu wanu, ndi anthu ake Israele.


Ndipo iwe Ezara monga mwa nzeru za Mulungu wako ili m'dzanja lako, uike nduna, ndi oweruza milandu, aweruze anthu onse ali tsidya lija la mtsinje, onse akudziwa malamulo a Mulungu wako; ndi wosawadziwayo umphunzitse.


Naimirira poima pao, nawerenga m'buku la chilamulo cha Yehova Mulungu wao limodzi la magawo anai a tsiku; ndi limodzi la magawo anai anawulula, napembedza Yehova Mulungu wao.


Idzani ananu ndimvereni ine, ndidzakulangizani zakumuopa Yehova.


Pomwepo ndidzalangiza ochimwa njira zanu; ndipo olakwa adzabwera kwa Inu.


Ine Mlaliki ndinali mfumu ya Israele mu Yerusalemu.


Ndipo mafumu adzakulera, ndi akazi ao aakulu adzakuyamwitsa; iwo adzakugwadira ndi nkhope zao zoyang'ana pansi, nadzaseteka fumbi la m'mapazi ako: ndipo iwe udzadziwa kuti Ine ndine Yehova, ndi iwo amene alindira Ine sadzakhala ndi manyazi.


natenge miyala ina, naikhazike m'malo mwa miyala ija; natenge dothi lina, namatenso nyumbayo.


Wa Isakara, Netanele mwana wa Zuwara.


Ndipo Yesu anayendayenda mu Galileya monse, analikuphunzitsa m'masunagoge mwao, nalalikira Uthenga Wabwino wa Ufumu, nachiritsa nthenda zonse ndi kudwala konse mwa anthu.


Ndipo anawaphunzitsa zinthu zambiri m'mafanizo, nanena nao m'chiphunzitso chake,


Taonani Teofilo inu, mau aja oyamba ndinakonza, za zonse Yesu anayamba kuzichita ndi kuziphunzitsa,


Adzaphunzitsa Yakobo maweruzo anu, ndi Israele chilamulo chanu; adzaika chofukiza pamaso panu, ndi nsembe yopsereza yamphumphu paguwa la nsembe lanu.


Taonani, ndinakuphunzitsani malemba ndi maweruzo, monga Yehova Mulungu wanga anandiuza ine, kuti muzichita chotero pakati padziko limene munkako kulilandira likhale lanulanu.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa