2 Mbiri 17:6 - Buku Lopatulika6 Ndi mtima wake unakwezeka m'njira za Yehova; anachotsanso misanje ndi zifanizo mu Yuda. Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 20146 Ndi mtima wake unakwezeka m'njira za Yehova; anachotsanso misanje ndi zifanizo m'Yuda. Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa6 Iyeyo adalimba mtima pa zinthu za Chauta. Kuwonjezera pamenepo, adathetsa akachisi ndiponso mafano a Aserimu ku Yuda. Onani mutuwoMawu a Mulungu mu Chichewa Chalero6 Mtima wake anawupereka kutsatira Yehova, kuwonjezera apo, anachotsa malo onse achipembedzo ndi mafano a Asera mu Yuda. Onani mutuwo |
Chitatha ichi chonse tsono, Aisraele onse opezekako anatuluka kunka kumizinda ya Yuda, naphwanya zoimiritsa, nalikha zifanizo, nagamula misanje ndi maguwa a nsembe mu Yuda monse, ndi mu Benjamini, mu Efuremunso, ndi mu Manase, mpaka adaziononga zonse. Pamenepo ana onse a Israele anabwerera, yense kudziko lake ndi kumizinda yao.