Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




2 Mbiri 17:14 - Buku Lopatulika

14 Kuwerenga kwao monga mwa nyumba za atate ao ndiko: a Yuda, akulu a zikwi; Adina wamkulu, ndi pamodzi ndi iye ngwazi zamphamvu zikwi mazana atatu;

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

14 Kuwerenga kwao monga mwa nyumba za atate ao ndiko: a Yuda, akulu a zikwi; Adina wamkulu, ndi pamodzi ndi iye ngwazi zamphamvu zikwi mazana atatu;

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

14 Chiŵerengero chao potsata mabanja ao chinali chotere: Ku Yuda, atsogoleri a zikwi anali aŵa: Adina amene anali ndi anthu amphamvu ndi olimba mtima 300,000.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

14 Chiwerengero chawo potsata mabanja awo chinali chotere: kuchokera ku Yuda, atsogoleri a magulu 1,000; mtsogoleri Adina, anali ndi anthu 300,000 odziwa nkhondo;

Onani mutuwo Koperani




2 Mbiri 17:14
11 Mawu Ofanana  

ndipo ndidzakuyesa iwe mtundu waukulu, ndipo ndidzakudalitsa iwe, ndi kubukitsa dzina lako; nukhale iwe mdalitso;


Ndipo ndidzayesa mbeu yako monga fumbi lapansi: chotere kuti ngati munthu angathe kuwerenga fumbi lapansi, chomwechonso mbeu yako idzawerengedwa.


Ndipo anamtulutsa iye kunja, nati, Tayang'anatu kumwamba, uwerenge nyenyezi, ngati ukhoza kuziwerenga zimenezo: ndipo anati kwa iye, Zoterezo zidzakhala mbeu zako.


Ndipo atafika ku Yerusalemu Rehobowamu, anamemeza a nyumba ya Yuda ndi Benjamini amuna osankhika zikwi zana limodzi mphambu makumi asanu ndi atatu, ndiwo ankhondo, alimbane ndi Aisraele kubwezanso ufumu kwa Rehobowamu.


Ndipo Abiya anayambana nkhondo ali ndi khamu la ngwazi za nkhondo, amuna osankhika zikwi mazana anai; Yerobowamu atandandalitsa nkhondo yake ilimbane naye ndi amuna osankhika zikwi mazana asanu ndi atatu, ndiwo ngwazi zamphamvu.


Ndipo Asa anali nao ankhondo ogwira zikopa ndi mikondo, a mu Yuda zikwi mazana atatu; ndi a mu Benjamini ogwira malihawo ndi okoka mauta zikwi mazana awiri mphambu makumi asanu ndi atatu; onsewo ngwazi zamphamvu.


Nakhala nazo ntchito zambiri m'mizinda ya Yuda, ndi anthu a nkhondo, ngwazi zamphamvu mu Yerusalemu.


ndi wotsatana naye mkulu Yehohanani, ndi pamodzi ndi iye zikwi mazana awiri mphambu makumi asanu ndi atatu;


Ndipo m'dzanja mwao munali khamu la nkhondo zikwi mazana atatu mphambu zikwi zisanu ndi ziwiri kudza mazana asanu ochita nkhondo ndi mphamvu yaikulu, kuthandiza mfumu alimbane ndi adani.


nasonkhanitsa khamu lonse tsiku loyamba la mwezi wachiwiri, ndipo iwo anawakumbira magwero ao kutchula mabanja ao, ndi nyumba za makolo ao, ndi kuwerenga maina kuyambira a zaka makumi awiri ndi mphambu mmodzimmodzi.


Werenga khamu lonse la ana a Israele, monga mwa mabanja ao, monga mwa nyumba ya makolo ao ndi kuwerenga maina ao, amuna onse mmodzimmodzi.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa