Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




2 Mbiri 17:12 - Buku Lopatulika

12 Ndipo Yehosafati anakula chikulire, namanga mu Yuda nyumba zansanja, ndi mizinda ya chuma.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

12 Ndipo Yehosafati anakula chikulire, namanga m'Yuda nyumba zansanja, ndi midzi ya chuma.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

12 Ndipo mphamvu za Yehosafati zidanka zikulirakulira. Ku Yuda adamanga malinga ndi mizinda yosungirako zinthu.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

12 Mphamvu za Yehosafati zinkakulirakulira. Iye anamanga malo otetezedwa ndi mizinda yosungiramo chuma mu Yuda

Onani mutuwo Koperani




2 Mbiri 17:12
13 Mawu Ofanana  

Ndipo Yehova anakuza Solomoni kwakukulu pamaso pa Aisraele onse, nampatsa ulemerero wachifumu, wakuti, asanakhale iyeyu, panalibe mfumu ya Israele inali nao wotero.


Ndipo Afilisti ena anabwera nazo kwa Yehosafati mitulo, ndi ndalama za msonkho; Aarabu omwe anabwera nazo kwa iye zoweta, nkhosa zamphongo zikwi zisanu ndi ziwiri mphambu mazana asanu ndi awiri ndi atonde zikwi zisanu ndi ziwiri mphambu mazana asanu ndi awiri.


Nakhala nazo ntchito zambiri m'mizinda ya Yuda, ndi anthu a nkhondo, ngwazi zamphamvu mu Yerusalemu.


Yehosafati tsono anali nacho chuma ndi ulemu zomchulukira, nachita chibale ndi Ahabu.


Namanga nsanja m'chipululu, nakumba zitsime zambiri; popeza anali nazo zoweta zambiri; kumadambo, ndi kuzidikha; nakhala nao olima minda, ndi osunga mpesa kumapiri ndi kunthaka yopatsa bwino; pakuti anakonda kulima.


Namanga mizinda m'mapiri a Yuda, ndi m'nkhalango anamanga nyumba zansanja, ndi nsanja zomwe.


Ndipo analimbika mtima, namangitsa linga lonse mopasuka, nalikweza mpaka pansanja, ndi linga lina kunja kwake, nalimbitsa Milo m'mzinda wa Davide, napanga zida ndi zikopa zochuluka.


Potero anawaikira akulu a misonkho kuti awasautse ndi akatundu ao. Ndipo anammangira Farao mizinda yosungiramo chuma, ndiyo Pitomu ndi Ramsesi.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa