Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




2 Mbiri 16:8 - Buku Lopatulika

8 Nanga Akusi ndi Alibiya, sanakhale khamu lalikulukulu, ndi magaleta ndi apakavalo ambirimbiri, koma muja munatama Yehova anawapereka m'dzanja mwanu?

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

8 Nanga Akusi ndi Alibiya, sanakhale khamu lalikulukulu, ndi magaleta ndi apakavalo ambirimbiri, koma muja munatama Yehova anawapereka m'dzanja mwanu?

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

8 Kodi Aetiopiya ndi Alibiya sanali gulu lalikulu lankhondo, lokhala ndi magaleta ochuluka ndiponso anthu ambirimbiri okwera pa akavalo? Komabe chifukwa chodalira Chauta, Chautayo adaŵapereka kwa inu.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

8 Kodi Akusi ndi Alibiya sanali gulu lankhondo lamphamvu lokhala ndi magaleta ochuluka ndi okwera magaleta ake? Koma pamene inu munadalira Yehova, Iye anawapereka mʼdzanja lanu.

Onani mutuwo Koperani




2 Mbiri 16:8
11 Mawu Ofanana  

Anakwera ndi magaleta chikwi chimodzi mphambu mazana awiri, ndi apakavalo zikwi makumi asanu ndi limodzi, ndi anthu adadza naye kutuluka mu Ejipito ngosawerengeka, Alibiya, Asuki, ndi Akusi.


Ndipo ana a Israele anathawa pamaso pa Yuda, nawapereka Mulungu m'dzanja lao.


Momwemo anachepetsedwa ana a Israele nthawi ija, napambana ana a Yuda; popeza anatama Yehova Mulungu wa makolo ao.


Ndipo Asa anali nao ankhondo ogwira zikopa ndi mikondo, a mu Yuda zikwi mazana atatu; ndi a mu Benjamini ogwira malihawo ndi okoka mauta zikwi mazana awiri mphambu makumi asanu ndi atatu; onsewo ngwazi zamphamvu.


Nthawi yomweyi Hanani mlauli anadza kwa Asa mfumu ya Yuda, nanena naye, Popeza mwatama mfumu ya Aramu, osatama Yehova Mulungu wanu, chifukwa chake khamu la nkhondo la mfumu ya Aramu lapulumuka m'dzanja lanu.


Pakuti khamu la nkhondo la Aaramu linadza la anthu owerengeka; ndipo Yehova anapereka khamu lalikulu m'dzanja lao; popeza adasiya Yehova Mulungu wa makolo ao. Motero anachitira Yowasi zomlanga.


limene litumiza mithenga pamtsinje m'ngalawa zamagumbwa zoyenda m'madzi, ndi kuti, Mukani, inu mithenga yoyenda msangamsanga kumtundu wa anthu aatali ndi osalala, kwa mtundu woopsa chikhalire chao, mtundu umene uyesa dziko ndi kupondereza pansi, umene dziko lake nyanja ziligawa!


Kusi ndi Ejipito ndiwo mphamvu yake, ndiyo yosatha, Puti ndi Libiya ndiwo akukuthandiza.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa