Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




2 Mbiri 16:4 - Buku Lopatulika

4 Ndipo Benihadadi anamvera mfumu Asa natumiza akazembe a magulu ake a nkhondo ayambane ndi mizinda ya Israele, nakantha Iyoni, ndi Dani, ndi Abele-Maimu, ndi mizinda yonse ya chuma ya Nafutali.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

4 Ndipo Benihadadi anamvera mfumu Asa natumiza akazembe a magulu ake a nkhondo ayambane ndi midzi ya Israele, nakantha Iyoni, ndi Dani, ndi Abele-Maimu, ndi midzi yonse ya chuma ya Nafutali.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

4 Benihadadi adamvera zimene adanena mfumu Asa zija, motero adatuma atsogoleri a magulu ake ankhondo kukathira nkhondo mizinda ya ku Israele. Adagonjetsa Iyoni, Dani, Abele-Maimu ndi mizinda yonse ya ku Nafutali yosungiramo zinthu.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

4 Beni-Hadadi anagwirizana ndi mfumu Asa ndipo anatumiza olamulira nkhondo ake kukathira nkhondo mizinda ya Israeli. Iwo anagonjetsa Iyoni, Dani, Abeli-Maimu ndi mizinda yonse yosungira chuma ya Nafutali.

Onani mutuwo Koperani




2 Mbiri 16:4
14 Mawu Ofanana  

Pamene anamva Abramu kuti mphwake anagwidwa, anatuluka natsogolera anyamata ake opangika, obadwa kunyumba kwake, mazana atatu kudza khumi ndi asanu ndi atatu, nawalondola kufikira ku Dani.


Ndipo Benihadadi anamvera mfumu Asa, natuma akazembe a nkhondo ake kukathira nkhondo kumizinda ya Israele, napasula Iyoni, ndi Dani, ndi Abele-Beti-Maaka, ndi Kineroti wonse, ndi dziko lonse la Nafutali.


ndi mizinda yonse yosungamo zinthu zake za Solomoni, ndi mizinda yosungamo magaleta ake, ndi mizinda yokhalamo apakavalo ake, ndi zina zilizonse zidakomera Solomoni kuzimanga mu Yerusalemu, ndi ku Lebanoni, ndi m'dziko lonse la ufumu wake.


Nimmvera mfumu ya Asiriya, nikwera kunka ku Damasiko mfumu ya Asiriya, niulanda, nipita nao anthu ake andende ku Kiri, nimupha Rezini.


Pakhale pangano pakati pa ine ndi inu, monga pakati pa atate wanga ndi atate wanu; taonani, ndakutumizirani siliva ndi golide; mukani, pasulani pangano lanu ndi Baasa mfumu ya Israele, kuti andichokere.


Ndipo kunali, pakumva ichi Baasa, analeka kumangitsa Rama, naleketsa ntchito yake.


Ndipo Yehosafati anakula chikulire, namanga mu Yuda nyumba zansanja, ndi mizinda ya chuma.


ndi Baalati, ndi mizinda yonse yosungiramo chuma anali nayo Solomoni, ndi mizinda yonse ya magaleta ake, ndi mizinda ya apakavalo ake, ndi zonse anazifuna Solomoni kuzimanga zomkondweretsa mu Yerusalemu, ndi mu Lebanoni, ndi m'dziko lonse la ufumu wake.


Potero anawaikira akulu a misonkho kuti awasautse ndi akatundu ao. Ndipo anammangira Farao mizinda yosungiramo chuma, ndiyo Pitomu ndi Ramsesi.


Koma kumene kunali nsautso sikudzakhala kuziya. Poyamba paja Mulungu ananyozetsa dziko la Zebuloni, ndi dziko la Nafutali, koma potsiriza pake Iye analichitira ulemu, pa khwalala la kunyanja, patsidya pa Yordani, Galileya wa amitundu.


Pakuti muzu wa zoipa zonse ndiwo chikondi cha pa ndalama; chimene ena pochikhumba, anasochera, nataya chikhulupiriro, nadzipyoza ndi zowawa zambiri.


posiya njira yolunjika, anasokera, atatsata njira ya Balamu mwana wa Beori, amene anakonda mphotho ya chosalungama;


Pamenepo anatuluka ana onse a Israele, nuunjikana msonkhano kwa Yehova ku Mizipa ngati munthu mmodzi, kuyambira ku Dani mpaka Beereseba ndi dziko la Giliyadi lomwe.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa